Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| “Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli. |
| 2 |
| Uzinena kuti, “ ‘Amayi ako anali ndani? Anali ngati mkango waukazi! Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna; unkalera ana ake pakati pa misona. |
| 3 |
| Unalera mmodzi mwa ana ake, ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama, ndipo unayamba kudya anthu. |
| 4 |
| Anthu amitundu anamva za mkangowo, ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo. Iwo anawukoka ndi ngowe kupita nawo ku dziko la Igupto. |
| 5 |
| “ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera, amayiwo anatenganso mwana wina namusandutsa mkango wamphamvu. |
| 6 |
| Unkayendayenda pakati pa mikango inzake, pakuti tsopano unali mkango wamphamvu. Unaphunzira kugwira nyama ndipo unayamba kudya anthu. |
| 7 |
| Unagwetsa malinga awo, ndikuwononga mizinda yawo. Onse a mʼdzikomo anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake. |
| 8 |
| Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira, inabwera kudzalimbana nawo. Anawutchera ukonde wawo, ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo. |
| 9 |
| Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga. Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso ku mapiri a Israeli. |
| 10 |
| “ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa wodzalidwa mʼmbali mwa madzi. Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa cha kuchuluka kwa madzi. |
| 11 |
| Nthambi zake zinali zolimba, zoyenera kupangira ndodo yaufumu. Unatalika nusomphoka pakati pa zomera zina. Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake, ndi nthambi zake zambiri. |
| 12 |
| Koma unazulidwa mwaukali ndipo unagwetsedwa pansi. Unawuma ndi mphepo ya kummawa, zipatso zake zinayoyoka; nthambi zake zolimba zinafota ndipo moto unapsereza mtengo wonse. |
| 13 |
| Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu, dziko lowuma ndi lopanda madzi. |
| 14 |
| Moto unatulukanso mu mtengomo ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake. Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo yoyenera kupangira ndodo yaufumu. Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/ezekiel/019.mp3
48
19