Wobadwa ndi munthu iwe, popeza Turo ananyodola Yerusalemu, ndi kuti, Onyo, watyoka uwu udali cipata ca mitundu ya anthu; wanditembenukira ine; ndidzakhuta ine, wapasuka uwu;
Pakuti atero Ambuye Yehova, Taona ndidzafikitsira Turo Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo, mfumu ya mafumu, yocokera kumpoto ndi akavalo, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi msonkhano wa anthu ambiri.
Papeza acuruka akavalo ace, pfumbi lao lidzakukuta; malinga ako adzagwedezeka ndi phokoso la apakavalo, ndi njinga za magareta, palowa iye pa zipata zako, monga umo amalowera m'mudzi popasukira linga lace.
Ndipo adzalanda cuma cako ndi kufunkha malonda ako, nadzagwetsa malinga ako ndi kupasula nyumba zako zofunika, nadzaponya miyala yako, ndi mitengo yako, ndi pfumbi lako, m'madzi.
Ndipo adzakukwezera nyimbo ya maliro, ndi kunena nawe, Watayika bwanji, ndiwe pakhala pa anthu a panyanja, mudzi womveka, unalimbika panyanja, uwo ndi okhalamo, amene anakhalitsa kuopsa kwao pa onse okhala momwemo!
pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa ku malo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,