Ku mayambiriro a chaka, tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 25 cha ukapolo wathu, ndiye kuti patapita zaka khumi ndi zinai Yerusalemu ataonongedwa, dzanja la Chauta lidandigwira nkupita nane ku Yerusalemu.
Panalinso zipinda za alonda, ndipo chilichonse chinali bango lathunthu m'litali mwake, chimodzimodzinso mu ufupi mwake, bango lathunthu. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita aŵiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pachipata pafupi ndi khonde lam'kati lapachipata, chinali bango lathunthu.
M'kati mwa chipata chakuvumacho munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zolingana, ndipo mphuthu zake pa mbali zonse zinali zolingananso.
Kumaso kwa zipinda za alonda zija kunali kachipupa ka mita limodzi m'litali mwake ndi muufupi momwe. Zipinda zitatuzo zinali za mamita atatu mbali zonse.
Tsono adayesa kutalika kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china, kuchokera ku chitseko mpaka kuchitseko china. Kutalika kwake kunali mamita 12 ndi theka.
Makoma a zipinda zija ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lam'kati linali nawonso mazenera m'kati mwake. Pa makoma onse adaazokotapo zithunzi za kanjedza.
Tsono adayesa m'kati mwa bwalo kuchokera ku chipata cham'munsi mpaka ku chipata chakunja cha bwalo lam'kati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Zipinda za alonda zimene zinali zitatu pa mbali iliyonse, mphuthu zake ndiponso khonde lake lam'kati, zonse zinali zolingana ndi za chipata choyamba chija. M'litali mwake chinali mamita 25, ndipo muufupi mwake chinali mamita 12 ndi theka.
Chipata chonga chakuvuma chija chidakaloŵa ku bwalo lam'kati moyang'anana ndi chipata chakumpoto. Adachiyesa kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china, kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja, ndipo pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku. Linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Khonde lake lam'kati lidaayang'ana bwalo lakunja. Pa mphuthu zake adaazokotapo zithunzi za kanjedza uku ndi uku, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Chipinda choyang'ana kumpotochi ncha ansembe oyang'anira za guwa lansembe. Ameneŵa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene angafike kufupi kudzatumikira Chauta.
“Tsono munthu uja adayesa bwalolo, linali lolingana m'litali ndi muufupi mwake, mamita 50 mbali iliyonse. Ndipo guwa linali kumaso kwa Nyumba ya Mulungu.
Pambuyo pake adapita nane m'khonde lam'kati la Nyumba ya Mulunguyo. Adayesa mphuthu za khondelo zinali za mamita aŵiri ndi theka mbali zonse. Muufupi mwake mwa chipata munali mamita asanu ndi aŵiri. Zipupa za pambali pa chipata zinali za mita limodzi ndi theka mbali zonse.