Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto. |
| 2 |
| Cakuno ca m'litali mwace mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwace mikono makumi asanu. |
| 3 |
| Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri. |
| 4 |
| Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwace mikono khumi m'kati mwace, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto. |
| 5 |
| Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda. |
| 6 |
| Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; cifukwa cace zam'mwambazo zinacepa koposa zakunsi ndi zapakati kuyambira pansi. |
| 7 |
| Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu. |
| 8 |
| Pakuti kupingasa kwace kwa nyumba yazipinda inali m'bwalo lakunja, kunali mikono makumi asanu; ndipo taonani, kuloza ku khomo la Kacisi inali mikono zana limodzi. |
| 9 |
| Ndipo pansi pa zipinda izi panali polowera mbali ya kum'mawa, poloweramo kucoka ku bwalo lakunja. |
| 10 |
| M'kucindikira kwa linga la bwalo, kuloza kumwera, cakuno ca mpatawo, cakuno ca nyumba, panali nyumba yazipinda. |
| 11 |
| Ndipo njira ya pakhomo pao inanga maonekedwe a njira ya ku nyumba yazipinda yoloza kumpoto, inalingana nayo m'litali mwace, momwemonso kupingasa kwace; ndi m'maturukiro mwace monse munali monga mwa macitidwe a inzace, ndi monga mwa makomo a inzace. |
| 12 |
| Ndi monga mwa makomo a zipinda za kumwela panali khomo polekeza njira, ndiyo njira yokhudzana ndi linga la kum'mawa polowamo. |
| 13 |
| Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwela, ziri cakuno ca mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulikitsa; kumeneko aziika zopatulikitsa, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yaucimo, ndi nsembe yoparamula; pakuti malowo ndi opatulika. |
| 14 |
| Atalowa ansembe asaturukenso m'malo opatulika kumka ku bwalo lakunja, koma komweko aziika zobvala zao zimene atumikira nazo; pakuti ziri zopatulika; ndipo abvale zobvala zina, nayandikire zinthu wamba za anthu. |
| 15 |
| Atatha tsono kuyesa nyumba ya m'katimo, anaturuka nane njira ya cipata coloza kum'mawa, nayesa bwalo pozungulira pace. |
| 16 |
| Anayesa mbali ya kum'mawa ndi bango loyesera, mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace. |
| 17 |
| Anayesa mbali ya kumpoto mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, pozungulira pace. |
| 18 |
| Anayesa mbali ya kumwela mabango mazana asanu, kuyesa ndi bango loyesera, |
| 19 |
| Anatembenukira ku mbali ya kumadzulo, nayesa mabango mazana asanu ndi bango loyesera. |
| 20 |
| Analiyesa mbali zace zinai, linali nalo linga pozungulira pace, utali wace mazana asanu, citando cace mazana asanu, kusiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zawamba. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/ezekiel/042.mp3
48
42