|
| 1 |
|
| Efraimu akudya mphepo, natsata mphepo ya kum'mawa; tsiku lonse acurukitsa mabodza ndi cipasuko, ndipo acita pangano ndi Asuri, natenga mafuta kumka nao ku Aigupto, |
|
| 2 |
|
| Ndipo Yehova ali ndi mlandu ndi Yuda, nadzalanga Yakobo monga mwa njira zace, adzambwezera monga mwa macitidwe ace. |
|
| 3 |
|
| M'mimba anagwira ku citende ca mkuru wace, ndipo atakula mphamvu analimbana ndi Mulungu; |
|
| 4 |
|
| inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Beteli, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife; |
|
| 5 |
|
| ndiye Yehova Mulungu wa makamu, cikumbukilo cace ndi Yehova. |
|
| 6 |
|
| M'mwemo utembenukire kwa Mulungu wako, sunga cifundo ndi ciweruzo, nuyembekezere Mulungu wako kosalekeza. |
|
| 7 |
|
| Ndiye Mkanani, m'dzanja lace muli miyeso yonyenga, akonda kusautsa. |
|
| 8 |
|
| Ndipo Efraimu anati, Zedi ndasanduka wolemera, ndadzionera cuma m'nchito zonse ndinazigwira; sadzapeza mwa ine mphulupulu yokhala cimo. |
|
| 9 |
|
| Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere dziko la Aigupto, ndidzakukhalitsanso m'mahema, monga masiku a masonkhano oikika. |
|
| 10 |
|
| Ndalankhulanso ndi aneneri, ndipo Ine ndacurukitsa masomphenya; ndi pa dzanja la aneneri ndinanena ndi mafanizo. |
|
| 11 |
|
| Kodi Gileadi ndiye wopanda pace? akhala acabe konse; m'Giligala aphera nsembe yang'ombe; inde maguwa ao a nsembe akunga miulu yamiyala m'micera ya munda. |
|
| 12 |
|
| Ndipo Yakobo anathawira ku thengo la Aramu, ndi Israyeli anagwira nchito cifukwa ca mkazi, ndi cifukwa ca mkazi anaweta nkhosa. |
|
| 13 |
|
| Ndipo mwa mneneri Yehova anakweretsa Israyeli kucokera m'Aigupto, ndi mwa mneneri anasungika. |
|
| 14 |
|
| Efraimu wautsa mkwiyo wowawa, m'mwemo Iye adzamsiyira mwazi wace, ndi Ambuye wace adzambwezera comtonza cace. |
|
|
|
|