Lankhula ndi ana a lsrayeli, nunene nao, Ali yense mwa inu akabwera naco copereka ca kwa Yehova, muzibwera naco copereka canu cikhale ca zoweta, ca ng'ombe, kapena ca nkhosa, kapena ca mbuzi.
Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira pa guwa la nsembe, lokhala pa khoma la cihema cokomanako.
koma atsuke ndi madzi matumbo ace ndi miyendo yace; ndi wansembe atenthe zonsezi pa guwa la nsembe, zikhale nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wace pa guwa la nsembe pozungulira.
Koma atsuke ndi madzi matumbo ndi miyendo; ndi wansembe abwere nazo zonse nazitenthe pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.
nang'ambe mapiko ace osawacotsa konse ai; ndipo wansembeyo aitenthe pa guwa la nsembe, pa nkhuni ziri pamoto; ndiyo nsembe yopsereza, nsembe yamoto, ya pfungo lokoma la kwa Yehova.