|
| 1 |
| Izi ndi zimene Obadiya adaona m'masomphenya. Naŵa mau a Ambuye Chauta onena za Aedomu. Chauta adatuma wamthenga wake kwa anthu a mitundu yonse, ndipo tidamva mau ake, adati, “Konzekani, tiyeni tikamenyane nkhondo ndi Aedomu.” |
| 2 |
| Chauta akuuza Aedomu kuti, “Ndithu ndidzakutsitsani kotheratu, anthu a mitundu yonse adzakunyozani kwambiri. |
| 3 |
| Mwanyengedwa ndi mtima wanu wonyada. Likulu lanu lili pakati pa matanthwe, mumakhala pa mapiri aatali. Mumanena kuti, ‘Ndani angatitsitse pansi?’ |
| 4 |
| Komatu ngakhale muuluke pamwamba ngati chiwombankhanga, ngakhale mumange chisa chanu pakati pa nyenyezi, ndidzakutsitsanibe pansi.” Akutero Chauta. |
| 5 |
| “Akuba akabwera usiku, amangotengako zimene akufuna. Okolola akamathyola zipatso, amasiyako zina. Koma inuyo adani anu akupululani kotheratu. |
| 6 |
| Onani m'mene alisakazira dziko la Esau, ndi m'mene achifunkhira chuma chake chonse. |
| 7 |
| Ogwirizana nanu akunyengani, akupirikitsani m'dziko mwanu. Okuthandizani pa nkhondo akugonjetsani. Abwenzi anu apamtima akutcherani msampha, mwathedwa nzeru tsopano.” |
| 8 |
| Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzaononga anzeru onse a ku Edomu, ndidzathetsa kuchenjera konse kwa zidzukulu za Esau. |
| 9 |
| Ngwazi za ku Temani zidzachita mantha, ankhondo onse adzaphedwa ku mapiri a Esau. |
| 10 |
| “Aedomu inu, chifukwa cha zankhanza zimene mudachita abale anu, zidzukulu za Yakobe, adzakuchititsani manyazi ndi kukuwonongani mpaka muyaya. |
| 11 |
| Munkangoonerera pamene adani ankaŵalanda chuma chao, munkachita ngati kuvomerezana nawo, amene ankaloŵa pa zipata za Yerusalemu, namagaŵana chumacho. |
| 12 |
| Inu simukadayenera kuŵanyodola abale anu Ayuda chifukwa cha tsoka lao. Simukadayenera kukondwerera kuwonongeka kwao. Simukadayenera kuŵaseka pamene iwo anali m'mavuto. |
| 13 |
| Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuloŵa mu mzinda wa anthu anga. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kuŵanyodola. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kulanda chuma chao. |
| 14 |
| Simukadayenera kudikira pa mphambano za miseu kuti mugwire anthu othaŵa. Pa tsiku lao la tsoka simukadayenera kupereka anthu ao otsala kwa adani. |
| 15 |
| “Posachedwapa lifika tsiku la Chauta pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena. Zimene mudachitazo zidzakubwererani. |
| 16 |
| Anthu anga adamwa chikho cha zoŵaŵa pa phiri langa loyera, koma mitundu ina ya anthu idzamwa chikho cha zoŵaŵa kopitirira. Idzachita kugugudiza chikhocho kenaka nkuzimirira pomwepo. |
| 17 |
| “Koma pa phiri la Ziyoni padzakhala ena opulumuka, ndipo phirilo lidzakhala loyera. Pamenepo fuko la Yakobe lidzalandira choloŵa chakechake. |
| 18 |
| Fuko la Yakobe lidzakhala ngati moto, fuko la Yosefe lidzakhala ngati malaŵi a moto, fuko la Esau lidzakhala ngati ziputu. Adzaŵatentha ndi kuŵapsereza, ndipo sipadzapulumuka munthu aliyense.” Akutero Chauta. |
| 19 |
| Ayuda akumwera adzalandira phiri la Esau, akuzambwe adzalandira dziko la Afilisti. Akumpoto adzalandira dziko la Efuremu ndi likulu lake Samariya, ndipo Abenjamini adzalandira dziko lakuvuma la Giliyadi. |
| 20 |
| Aisraele amene anali ku ukapolo adzalandira dziko la Kanani mpaka kumpoto ku Zarefati. A ku Yerusalemu amene anali ku ukapolo ku Sefaradi adzalandira mizinda yakumwera ku Negebu. |
| 21 |
| Ngwazi zochokera ku Yerusalemu zidzagonjetsa ndi kumalamulira dziko la Edomu ndipo ufumu wonse udzakhala wa Chauta. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/obadiah/001.mp3
1
1