|
| 1 |
|
| NDIPO mau a Yehova anadza kwa Yona mwana wa Amitai, ndi kuti, |
|
| 2 |
|
| Nyamuka, pita ku Nineve, mudzi waukuruwo, nulalikire motsutsana nao; pakuti coipa cao candikwerera pamaso panga. |
|
| 3 |
|
| Koma Yona ananyamuka kuti athawire ku Tarisi, kuzemba Yehova; ndipo anatsikira ku Yopa, napezako combo comuka ku Tarisi, napereka ndalama zace, natsikira m'menemo, kuti apite nao ku Tarisi kuzemba Yehova. |
|
| 4 |
|
| Koma Yehova anautsa cimphepo cacikuru panyanja, ndipo panali namondwe wamkuru panyanja, ndi combo cikadasweka. |
|
| 5 |
|
| Pamenepo amarinyero anacita mantha, napfuulira yense kwa mlungu wace, naponya m'nyanja akatundu anali m'combo kucipepuza. Koma Yona adatsikira m'munsi mwa combo, nagona tulo tofa nato. |
|
| 6 |
|
| Ndipo mwini combo anadza kwa iye, nanena naye, Utani iwe wam'tulo? uka, itana Mulungu wako, kapena Mulunguyo adzatikumbukila tingatayike. |
|
| 7 |
|
| Ndipo anati yense kwa mnzace, Tiyeni ticite maere, kuti tidziwe coipa ici catigwera cifukwa ca yani. M'mwemo anacita maere, ndipo maere anagwera Yona. |
|
| 8 |
|
| Pamenepo anati kwa iye, Utiuzetu coipa ici catigwera cifukwa ca yani? nchito yako njotani? ufuma kuti? dziko lako nliti? nanga mtundu wako? |
|
| 9 |
|
| Ndipo ananena nao, Ndine Mhebri, ndiopa Yehova Mulungu wa Kumwamba amene analenga nyanja ndi mtunda. |
|
| 10 |
|
| Pamenepo amunawo anaopa kwambiri, nati kwa iye, Ici nciani wacicita? Pakuti amunawo anadziwa kuti anathawa pamaso pa Yehova, popeza adawauza. |
|
| 11 |
|
| Tsono anati kwa iye, Ticitenji nawe, kuti nyanja iticitire bata? popeza namondwe anakula-kulabe panyanja. |
|
| 12 |
|
| Ndipo anati nao, Mundinyamule ndi kundiponya m'nyanja, momwemo nyanja idzacitira inu bata; pakuti ndidziwa kuti namondwe wamkuru amene wakugwerani cifukwa ca ine. |
|
| 13 |
|
| Koma amunawo anapalasa kubwerera kumtunda, koma sanathe; pakuti namondwe wa panyanja anakulakula mokomana nao. |
|
| 14 |
|
| Pamenepo anapfuulira kwa Yehova, nati, Tikupemphanitu, Yehova, tisatayike cifukwa ca moyo wa munthu uyu, musatisenzetse mwazi wosacimwa; pakuti, Inu Yehova, mwacita monga mudakomera Inu. |
|
| 15 |
|
| Momwemo ananyamula Yona, namponya m'nyanja; ndipo nyanja inaleka kukokoma kwace. |
|
| 16 |
|
| Ndipo amunawo anaopa Yehova ndi manthaakuru, namphera Yehova nsembe, nawinda. |
|
| 17 |
|
| Koma Yehova anaikiratu cinsomba cacikuru cimeze Yona; ndipo Yona anali m'miroba mwa nsombayi masiku atatu usana ndi usiku. |
|
|
|
|