Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoto. |
| 2 |
| Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani nchito yanu pakati pa zaka, Pakati pa zaka mudziwitse; Pa mkwiyo mukumbukile cifundo. |
| 3 |
| Mulungu anafuma ku Temani, Ndi Woyerayo ku phiri la Parana. Ulemerero wace unaphimba miyamba, Ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza. |
| 4 |
| Ndi kunyezimira kwace kunanga kuunika; Anali nayo mitsitsi ya dzuwa yoturuka m'dzanja lace. Ndi komweko kunabisika mphamvu yace. |
| 5 |
| Patsogolo pace panapita mliri, Ndi makara amoto anaturuka pa mapaziace. |
| 6 |
| Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; Anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; Ndi mapiri acikhalire anamwazika, Zitunda za kale lomwe zinawerama; Mayendedwe ace ndiwo a kale lomwe. |
| 7 |
| Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; Nsaru zocinga za dziko la Midyani zinanjenjemera. |
| 8 |
| Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, Kapena ukali wanu panyanja, Kuti munayenda pa akavalo anu, Pa magareta anu a cipulumutso? |
| 9 |
| Munapombosola uta wanu; Malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje. |
| 10 |
| Mapiri anakuonani, namva zawawa; Cigumula ca madzi cinapita; Madzi akuya anamveketsa mau ace, Nakweza manja ace m'mwamba. |
| 11 |
| Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; Pa kuunika kwa mibvi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira. |
| 12 |
| Munaponda dziko ndi kulunda, Munapuntha amitundu ndi mkwiyo. |
| 13 |
| Munaturukira cipulumutso ca anthu anu, Cipulumutso ca odzozedwa anu; Munakantha mutu wa nyumba yawoipa, Ndi kufukula maziko kufikira m'khosi. |
| 14 |
| Munapyoza ndi maluti ace mutu wa ankhondo ace; Anadza ngati kabvumvulu kundimwaza; Kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mabisika. |
| 15 |
| Munaponda panyanja ndi akavaloanu, Madzi amphamvu anaunjikana mulu. |
| 16 |
| Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, Milomo yanga inanthunthumira pamau, M'mafupa mwanga mudalowa cibvundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; Kuti ndipumule tsiku lamsauko, Pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu. |
| 17 |
| Cinkana mkuyu suphuka, Kungakhale kulibe zipatso kumpesa; Yalephera nchito ya azitona, Ndi m'minda m'mosapatsa cakudya; Ndi zoweta zacotsedwa kukhola, Palibenso ng'ombe m'makola mwao; |
| 18 |
| Koma ndidzakondwera mwa Yehova, Ndidzasekerera mwa Mulungu wa cipulumutso canga. |
| 19 |
| Yehova, Ambuye, ndiye mphamvuyanga, Asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, Nadzandipondetsa pa misanje yanga. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/habakkuk/003.mp3
3
3