Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Pemphero la Habakuku mneneri, pa Sigionoti. |
| 2 |
| Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo. |
| 3 |
| Mulungu anafuma ku Temani, ndi Woyerayo kuphiri la Parani. Ulemerero wake unaphimba miyamba, ndi dziko lapansi linadzala ndi kumlemekeza. |
| 4 |
| Ndi kunyezimira kwake kunanga kuunika; anali nayo mitsitsi ya dzuwa yotuluka m'dzanja lake, ndi komweko kunabisika mphamvu yake. |
| 5 |
| Patsogolo pake panapita mliri, ndi makala amoto anatuluka pa mapazi ake. |
| 6 |
| Anaimirira, nandengulitsa dziko lapansi; anapenya, nanjenjemeretsa amitundu; ndi mapiri achikhalire anamwazika, zitunda za kale lomwe zinawerama; mayendedwe ake ndiwo a kale lomwe. |
| 7 |
| Ndinaona mahema a Kusani ali mkusauka; nsalu zotchinga za dziko la Midiyani zinanjenjemera. |
| 8 |
| Kodi Yehova anaipidwa nayo mitsinje? Mkwiyo wanu unali pamitsinje kodi, kapena ukali wanu panyanja, kuti munayenda pa akavalo anu, pa magaleta anu a chipulumutso? |
| 9 |
| Munapombosola uta wanu; malumbiro analumbirira mafuko anali mau oona. Munang'amba dziko lapansi ndi mitsinje. |
| 10 |
| Mapiri anakuonani, namva zowawa; chigumula cha madzi chinapita; madzi akuya anamveketsa mau ake, nakweza manja ake m'mwamba. |
| 11 |
| Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira. |
| 12 |
| Munaponda dziko ndi kulunda, munapuntha amitundu ndi mkwiyo. |
| 13 |
| Munatulukira chipulumutso cha anthu anu, chipulumutso cha odzozedwa anu; munakantha mutu wa nyumba ya woipa, ndi kufukula maziko kufikira m'khosi. |
| 14 |
| Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika. |
| 15 |
| Munaponda panyanja ndi akavalo anu, madzi amphamvu anaunjikana mulu. |
| 16 |
| Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu. |
| 17 |
| Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao; |
| 18 |
| koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa. |
| 19 |
| Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga, asanduliza mapazi anga ngati a mbawala, nadzandipondetsa pa misanje yanga. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/habakkuk/003.mp3
3
3