Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Pemphero la mneneri Habakuku potsata mayimbidwe a Sigionoti. |
| 2 |
| Inu Yehova, ndamva za kutchuka kwanu; Inu Yehova, ntchito zanu zandiopsa. Muzichitenso masiku athu ano, masiku athu ano zidziwike; mu ukali wanu mukumbukire kuchita chifundo. |
| 3 |
| Mulungu anabwera kuchokera ku Temani, Woyerayo kuchokera ku Phiri la Parani. Sela Ulemerero wake unaphimba mlengalenga ndipo dziko lapansi linadzaza ndi matamando ake. |
| 4 |
| Kuwala kwa ulemerero wake kunali ngati kutuluka kwa dzuwa; kunyezimira kunkatuluka mʼdzanja lake, mʼmene anabisamo mphamvu zake. |
| 5 |
| Patsogolo pake pankagwa mliri; nthenda yoopsa inkagwa kumbuyo kwake. |
| 6 |
| Iye anayimirira ndi kugwedeza dziko lapansi; anayangʼana ndipo mitundu ya anthu inanjenjemera. Mapiri okhazikika anagumuka ndipo zitunda zakalekale zinatitimira. Njira zake ndi zachikhalire. |
| 7 |
| Ndinaona matenti a ku Kusani ali pa mavuto, mokhala a ku Midiyani muli ululu waukulu. |
| 8 |
| Inu Yehova, kodi munakwiyira mitsinje? Kodi munakalipira timitsinje? Kodi munapsera mtima nyanja pamene munakwera pa akavalo anu ndiponso magaleta anu achipulumutso? |
| 9 |
| Munasolola uta wanu mʼchimake, munayitanitsa mivi yambiri. Sela Munagawa dziko lapansi ndi mitsinje; |
| 10 |
| mapiri anakuonani ndipo anagwedezeka. Madzi amphamvu anasefukira; nyanja yozama inakokoma ndipo mafunde ake anakwera kwambiri. |
| 11 |
| Dzuwa ndi mwezi zinayima chilili mlengalenga, pa kungʼanima kwa mivi yanu yowulukayo, pa kunyezimira kwa mkondo wanu. |
| 12 |
| Munayendayenda mʼdziko lapansi muli ndi ukali, ndipo munapondereza mitundu ya anthu muli ndi mkwiyo. |
| 13 |
| Munapita kukalanditsa anthu anu, kukapulumutsa wodzozedwa wanu. Munakantha mtsogoleri wa dziko la anthu oyipa, munawononga anthu ake onse. Sela |
| 14 |
| Ndi mkondo wake womwe munalasa mtsogoleri wake pamene ankhondo ake anabwera mwamphamvu kudzatibalalitsa, ankasangalala ngati kuti akudzawononga osauka amene akubisala. |
| 15 |
| Munapondaponda pa nyanja ndi akavalo anu, kuvundula madzi amphamvu. |
| 16 |
| Ndinamva ndipo mtima wanga unagunda kwambiri, milomo yanga inanjenjemera pakumva phokosolo; mafupa anga anaguluka, ndipo mawondo anga anawombana. Komabe ndikuyembekezera mofatsa, tsiku la masautso limene lidzafike pa mtundu wa anthu umene ukutithira nkhondo. |
| 17 |
| Ngakhale mtengo wa mkuyu usachite maluwa, ndipo mipesa ikhale yopanda mphesa. Ngakhale mitengo ya olivi isabereke zipatso, ndipo mʼminda musatuluke kanthu. Ngakhale nkhosa ndi ngʼombe zithe mʼkhola, |
| 18 |
| komabe ine ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasangalala mwa Mulungu Mpulumutsi wanga. |
| 19 |
| Ambuye Yehova ndiye mphamvu yanga; amalimbitsa miyendo yanga ngati ya mbawala yayikazi, amandithandiza kukafika pamwamba pa phiri. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za nsambo. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/habakkuk/003.mp3
3
3