Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku la makumi awiri ndi cimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, |
| 2 |
| Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealitiyeli, ciwanga ca Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti, |
| 3 |
| Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wace woyamba? ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati cabe? |
| 4 |
| Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkuru wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kucita; pakui. Ine ndiri pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; |
| 5 |
| monga momwe ndinapangana nanu muja munaturuka m'Aigupto, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu. |
| 6 |
| Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; |
| 7 |
| ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu. |
| 8 |
| Siliva ndi wanga, golidi ndi wanga, ati Yehova wa makamu. |
| 9 |
| Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu. |
| 10 |
| Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wacisanu ndi cinai, caka caciwiri ca Dariyo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, |
| 11 |
| Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za cilamulo, ndi kuti, |
| 12 |
| Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena cakudya ciri conse, ndi ngudulira, kodi cisandulika copatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai. |
| 13 |
| Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa. |
| 14 |
| Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo nchito iri yonse ya manja ao; ndi ici acipereka, ciri codetsedwa. |
| 15 |
| Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kacisi wa Yehova, |
| 16 |
| pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku coponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha. |
| 17 |
| Ndinakukanthani ndi cinsikwi ndi cinoni ndi matalala m'nchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. |
| 18 |
| Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi cinai la mwezi wacisanu ndi cinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kacisi wa Yehova, samalirani. |
| 19 |
| Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi mzitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani. |
| 20 |
| Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yaciwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti, |
| 21 |
| Nena ndi Zerubabele ciwanga ca Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi; |
| 22 |
| ndipo ndidzagubuduza mipando yacifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magareta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wace. |
| 23 |
| Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealitiyeli, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/haggai/002.mp3
2
2