Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku la makumi awiri ndi chimodzi la mweziwo, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, |
| 2 |
| Unenetu kwa Zerubabele, mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa otsala a anthu, kuti, |
| 3 |
| Adatsala ndani mwa inu amene anaona nyumba iyi m'ulemerero wake woyamba? Ndipo muiona yotani tsopano? Kodi siikhala m'maso mwanu ngati chabe? |
| 4 |
| Koma limbika tsopano, Zerubabele, ati Yehova; ulimbikenso Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe; ndipo mulimbike inu nonse anthu a m'dziko, ati Yehova, ndi kuchita; pakuti Ine ndili pamodzi ndi inu, ati Yehova wa makamu; |
| 5 |
| monga momwe ndinapangana nanu muja munatuluka m'Ejipito, ndi Mzimu wanga unakhala pakati pa inu; musamaopa inu. |
| 6 |
| Pakuti atero Yehova wa makamu: Kamodzinso, katsala kanthawi, ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe; |
| 7 |
| ndipo ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wa makamu. |
| 8 |
| Siliva ndi wanga, ya golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu. |
| 9 |
| Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo, ati Yehova wa makamu; ndipo m'malo muno ndidzapatsa mtendere, ati Yehova wa makamu. |
| 10 |
| Tsiku la makumi awiri ndi anai la mwezi wachisanu ndi chinai, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza mwa Hagai mneneri, ndi kuti, |
| 11 |
| Atero Yehova wa makamu: Funsatu ansembe za chilamulo, ndi kuti, |
| 12 |
| Munthu akanyamulira nyama yopatulika m'ngudulira, nakhudza mkate, kapena ndiwo, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, ndi ngudulira, kodi chisandulika chopatulika? Ndipo ansembe anayankha nati, Iai. |
| 13 |
| Pamenepo Hagai anati, Munthu wodetsedwa ndi mtembo akakhudza kanthu ka izi, kodi kali kodetsedwa kanthuka? Ndipo ansembe anayankha nati, Kadzakhala kodetsedwa. |
| 14 |
| Ndipo Hagai anayankha, nati, Momwemo anthu awa, ndi momwemo mtundu uwu pamaso panga, ati Yehova; ndi momwemo ntchito iliyonse ya manja ao; ndi ichi achipereka, chili chodetsedwa. |
| 15 |
| Ndipo tsono, samalirani, kuyambira lero ndi m'tsogolomo, kuti, kusanaikidwe mwala pa mwala m'Kachisi wa Yehova, |
| 16 |
| pamenepo ponse munthu akadza ku mulu woyenera miyeso makumi awiri, pali khumi yokha; munthu akadza ku choponderamo mphesa kudzatunga mbiya makumi asanu, pali makumi awiri okha. |
| 17 |
| Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova. |
| 18 |
| Musamalire, kuyambira lero ndi m'tsogolo, kuyambira tsiku la makumi awiri ndi chinai la mwezi wachisanu ndi chinai, kuyambira tsiku lija anamanga maziko a Kachisi wa Yehova, samalirani. |
| 19 |
| Kodi mbeu ikali m'nkhokwe? Ngakhale mpesa, ndi mkuyu, ndi khangaza ndi azitona sizinabala; kuyambira lero lino ndidzakudalitsani. |
| 20 |
| Ndipo mau a Yehova anadza nthawi yachiwiri kwa Hagai tsiku la makumi awiri la mwezi, ndi kuti, |
| 21 |
| Nena ndi Zerubabele chiwanga cha Yuda, kuti, Ndidzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi; |
| 22 |
| ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake. |
| 23 |
| Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzakutenga, Zerubabele mtumiki wanga, mwana wa Sealatiele, ati Yehova, ndi kuika iwe ngati mphete yosindikizira; pakuti ndakusankha, ati Yehova wa makamu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/haggai/002.mp3
2
2