Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido, uthenga uwu wakuti,
Tsiku la 24 la mwezi wa khumi ndi umodzi, mwezi wa Sebati, chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, Chauta adapatsa uthenga mneneri Zekariya, mwana wa Berekiya, mdzukulu wa Ido. Tsono Zekariya adati,
Tsono mngelo wa Chautayo anafunsa kuti, ‘Inu Chauta Wamphamvuzonse, kodi Yerusalemu ndi mizinda ya ku Yuda imene mudaikwiyira pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, mudzakhalabe oiwumira mtima mpaka liti?’
Nchifukwa chake ndabwerera ku Yerusalemu ndi mtima wachifundo. Nyumba yanga adzaimanganso kumeneko, ndipo adzatenga chingwe choyesera kuti amangenso mzinda wa Yerusalemu,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Ndidafunsa mngelo amene ankalankhula nane tanthauzo lake la nyanga zimenezo. Iye adandiyankha kuti, ‘Zimenezi ndizo mphamvu zapansi pano zimene zidabalalitsa anthu a ku Yuda, a ku Israele ndi a ku Yerusalemu.’
Ine ndidafunsa kuti, ‘Kodi akudzachita chiyani?’ Iye adayankha kuti, ‘Mphamvu zijazi zidabalalitsa Yuda ndi Yerusalemu kotheratu, kotero kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woŵeramutsa mutu. Koma amisiri osulaŵa, abwera kudzaopsa ndi kudzaononga mphamvu za mitundu ya anthu imene idaagonjetsa dziko la Yuda, ndi kumwaza anthu ake.’ ”