Tsiku ilo, ati Yehova, ndidzakantha kavalo ali yense ndi kumdabwitsa, ndi womkwera adzayaluka; ndipo ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo ali yense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.
Tsiku ilo ndidzaika akalonga a Yuda ngati phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu; ndipo adzatha mitundu yonse ya anthu pozungulirapo, ku dzanja lamanja ndi lamanzere; ndipo Yerusalemu adzakhalanso m'malo mwace, m'Yerusalemu.
Tsiku ilo Yehova adzacinjiriza okhala m'Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala m'Yerusalemu, mzimu wa cisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wace mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wace woyamba.
Ndipo dziko lidzalira, banja liri lonse pa lokha; banja la nyumba ya Davide pa lokha, ndi akazi ao pa okha; banja la nyumba ya Natani pa lokha, ndi akazi ao pa okha;