Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Yehova anawuza Mose kuti, |
| 2 |
| “Tuma anthu kuti akazonde dziko la Kanaani limene ndikupereka kwa Aisraeli. Kuchokera pa fuko lililonse utume munthu mmodzi amene ndi mtsogoleri wawo.” |
| 3 |
| Monga mwa mawu a Yehova, Mose anawatuma kuchokera ku chipululu cha Parani. Onsewo anali atsogoleri a Aisraeli. |
| 4 |
| Mayina awo ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Samuwa mwana wa Zakuri; |
| 5 |
| kuchokera ku fuko la Simeoni, Safati mwana wa Hori; |
| 6 |
| kuchokera ku fuko la Yuda, Kalebe mwana wa Yefune; |
| 7 |
| kuchokera ku fuko la Isakara, Igala mwana wa Yosefe; |
| 8 |
| kuchokera ku fuko la Efereimu, Hoseya mwana wa Nuni; |
| 9 |
| kuchokera ku fuko la Benjamini, Paliti mwana wa Rafu; |
| 10 |
| kuchokera ku fuko la Zebuloni, Gadieli mwana wa Sodi; |
| 11 |
| kuchokera ku fuko la Manase (fuko la Yosefe), Gadi mwana wa Susi; |
| 12 |
| kuchokera ku fuko la Dani, Amieli mwana wa Gemali; |
| 13 |
| kuchokera ku fuko la Aseri, Seturi mwana wa Mikayeli; |
| 14 |
| kuchokera ku fuko la Nafutali, Naabi mwana wa Vofisi; |
| 15 |
| kuchokera ku fuko la Gadi, Geuweli mwana wa Maki. |
| 16 |
| Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa). |
| 17 |
| Mose atawatuma kuti akazonde Kanaani anati, “Mupite kudzera ku Negevi, mukapitirire mpaka ku dziko la mapiri. |
| 18 |
| Mukaone dzikolo kuti ndi lotani ndi anthu okhala mʼmenemo ngati ndi amphamvu kapena ofowoka, ochepa kapena ambiri. |
| 19 |
| Nanga dziko limene akukhalako ndi lotani? Ndi labwino kapena loyipa? Mizinda imene akukhalamo ndi yotani? Kodi ilibe malinga kapena ndi ya malinga? |
| 20 |
| Nthaka yake ndi yotani? Yachonde kapena yopanda chonde? Kodi dzikolo lili ndi mitengo kapena lilibe mitengo? Mukayesetse kubweretsako zipatso za mʼdzikomo.” (Inali nthawi yamphesa zoyamba kupsa). |
| 21 |
| Choncho anapita kukazonda dzikolo kuchokera ku chipululu cha Zini mpaka ku Rehobu, mopenyana ndi Lebo Hamati. |
| 22 |
| Anapita kudzera ku Negevi ndi kukafika ku Hebroni, kumene Ahimani, Sesai ndi Talimai, ana a Anaki ankakhala. (Anamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri asanamange Zowani ku Igupto). |
| 23 |
| Atafika ku chigwa cha Esikolo, anadulako nthambi ya mpesa ya phava limodzi la mphesa ndipo anthu awiri ananyamulizana, natenganso makangadza ndi nkhuyu. |
| 24 |
| Malo amenewo anawatcha chigwa cha Esikolo chifukwa cha phava la mphesa limene Aisraeli anadula kumeneko. |
| 25 |
| Patapita masiku makumi anayi, anthu aja anabwerako kokazonda dziko lija. |
| 26 |
| Ndipo atabwerako anapita kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa Aisraeli onse ku Kadesi mʼchipululu cha Parani. Kumeneko anafotokozera anthu onse nawaonetsanso zipatso za mʼdzikolo. |
| 27 |
| Anthuwo anafotokozera Mose kuti, “Tinapita ku dziko komwe munatituma. Dzikolo ndi loyenda mkaka ndi uchi ndipo zipatso zake ndi izi. |
| 28 |
| Koma anthu amene amakhala mʼdzikomo ndi amphamvu, mizinda yawo ndi ya malinga aakulu kwambiri. Tinaonanso Aanaki kumeneko. |
| 29 |
| Aamaleki amakhala ku Negevi, Ahiti, Ayebusi ndi Aamori amakhala mʼdziko la mapiri ndipo Akanaani amakhala pafupi ndi nyanja, mʼmbali mwa Yorodani.” |
| 30 |
| Koma Kalebe anawakhalitsa chete anthuwo pamaso pa Mose, ndipo anati, “Tiyeni tipite ndithu ndi kutenga dzikolo, pakuti tingathe kulitenga.” |
| 31 |
| Koma anthu aja amene anapita naye anati, “Sitingathe kulimbana ndi anthuwo popeza ndi amphamvu kuposa ifeyo.” |
| 32 |
| Choncho anthuwo anafalitsa pakati pa Aisraeli mbiri yoyipa ya dziko lomwe anakalionalo. Iwo anati, “Dziko limene tinapita kukalizonda limawononga anthu okhala mʼmenemo. Ndipo anthu onse amene tinakawaona kumeneko ndi ataliatali. |
| 33 |
| Kumeneko tinaona Anefili (ana a Aanaki ochokera kwa Nefili). Ifeyo timangodziona ngati ziwala mʼmaso mwawo, ndipo kwa iwo timaonekadi motero ndithu.” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/numbers/013.mp3
36
13