Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Yehova anawuza Mose kuti, |
| 2 |
| “Yankhula ndi Aisraeli ndipo akupatse ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse. Ulembe dzina la munthu aliyense pa ndodo yake. |
| 3 |
| Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse. |
| 4 |
| Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe. |
| 5 |
| Ndodo ya munthu amene ndamusankha idzachita maluwa potero ndidzaletsa madandawulo osatha a Aisraeli otsutsana nawe.” |
| 6 |
| Choncho Mose anayankhula ndi Aisraeli, ndipo atsogoleri awo anapereka ndodo khumi ndi ziwiri, imodzi kuchokera kwa mtsogoleri wa fuko lililonse ndipo ndodo ya Aaroni inali pakati pa ndodo zawozo. |
| 7 |
| Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano. |
| 8 |
| Pa tsiku lotsatira Mose analowa mu tenti ya msonkhanoyo ndipo anaona kuti ndodo ya Aaroni, yomwe inkayimira fuko la Levi, sinangophuka masamba chabe, komanso inachita maluwa nʼkubala zipatso za alimondi. |
| 9 |
| Choncho Mose anatulutsa ndodo zonse pamaso pa Yehova napita nazo kwa Aisraeli onse. Iwowo anaziona ndipo munthu aliyense anatenga ndodo yake. |
| 10 |
| Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.” |
| 11 |
| Mose anachita monga Yehova anamulamulira. |
| 12 |
| Aisraeli anati kwa Mose, “Tikufa! Tatayika, tonse tatayika! |
| 13 |
| Aliyense woyandikira chihema adzafa. Kodi ndiye kuti tonse tikufa?” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/numbers/017.mp3
36
17