Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati, |
| 2 |
| Ana a Israyeli azimanga mahema ao yense ku mbendera yace, ya cizindikilo ca nyumba ya kholo lace; amange mahema ao popenyana ndi cihema cokomanako pozungulira. |
| 3 |
| Ndipo iwo akumanga mahema ao ku m'mawa koturuka dzuwa ndiwo a mbendera ya cigono ca Yuda, monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Yuda ndiye Nahesoni mwana wa Aminadabu. |
| 4 |
| Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri, mphambu zinai, kudza mazana asanu ndi limodzi. |
| 5 |
| Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Isakara; ndipo kalonga wa ana a Isakara ndiye Netandi mwana wa Zuwara. |
| 6 |
| Ndipo khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zinai kudza mazana anai. |
| 7 |
| Ndi pfuko la Zebuloni: kalonga wa ana a Zebuloni ndiye Eliyabu mwana wa Heloni. |
| 8 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai. |
| 9 |
| Owerengedwa onse a cigono ca Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi cimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao, Ndiwo azitsogolera ulendo. |
| 10 |
| Mbendera ya cigono ca Rubeni ikhale kumwera monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Rubeni ndiye Elizuri mwana wa Sedeuri. |
| 11 |
| Ndi khamu lace, ndi olembedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu ndi cimodzi kudza mazana asanu. |
| 12 |
| Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Simeoni; ndi kalonga wa ana a Simeoni ndiye Selumiyeli mwana wa Surisadai. |
| 13 |
| Ndi khamu lace ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi zinai kudza mazana atatu. |
| 14 |
| Ndi pfuko la Gadi; kalonga wa ana a Gadi ndiye Eliyasafe mwana wa Reueli. |
| 15 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu. |
| 16 |
| Owerengedwa onse a cigono ca Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi cimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo. |
| 17 |
| Pamenepo khamu la Alevi azimuka naco cihema cokomanako, pakati pa makamu; monga amamanga mahema ao, momwemo azimuka ulendo wao, munthu yense pamalo pace, monga mwa mbendera zao. |
| 18 |
| Mbendera ya cigono ca Efraimu izikhala kumadzulo monga mwa makamu ao; ndipo kalonga wa ana a Efraimu ndiye Elisama mwana wa Amihudi. |
| 19 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai kudza mazana asanu. |
| 20 |
| Ndipo oyandikizana naye ndiwo a pfuko la Manase; ndi kalonga wa ana a Manase ndiye Gamaliyeli mwana wa Pedazuri. |
| 21 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana awiri. |
| 22 |
| Ndi pfuko la Benjamini: kalonga wa ana a Benjamini ndiye Abidana mwana wa Gideoni. |
| 23 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai. |
| 24 |
| Owerengedwa onse a cigono ca Efraimu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lacitatu paulendo. |
| 25 |
| Mbendera ya cigono ca Dani izikhala kumpoto monga mwa makamu ao; ndi kalonga wa ana a Dani ndiye Ahiyezeri mwana wa Amisadai. |
| 26 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri. |
| 27 |
| Ndipo iwo akumanga mahema ao poyandikizana naye ndiwo a pfuko la Aseri; ndi kalonga wa ana a Aseri ndiye Pagiyeli mwana wa Okirani. |
| 28 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi anai mphambu cimodzi kudza mazana asanu. |
| 29 |
| Ndi pfuko la Nafitali: ndi kalonga wa ana a Nafitali ndiye Ahira mwana wa Enani. |
| 30 |
| Ndi khamu lace, ndi owerengedwa ace, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. |
| 31 |
| Owerengedwa onse a cigono ca Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi Hmodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao. |
| 32 |
| Amenewo ndiwo anawerengedwa a ana a Israyeli monga mwa nyumba za makolo ao; owerengedwa onse a m'zigono, monga mwa makamu ao, ndiwo zikwi makumi khumi kasanu ndi kamodzi mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi makumi asanu. |
| 33 |
| Koma sanawerenga Alevi mwa ana a Israyeli; monga Yehova adauza Mose. |
| 34 |
| Ndipo ana a Israyeli anacita monga mwa zonse Yehova adauza Mose, momwemo anamanga mahema ao pa mbendera zao, momwemonso anayenda paulendo, yense monga mwa mabanja ace, monga mwa nyumba za makolo ace. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/numbers/002.mp3
36
2