Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zija zina, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu. |
| 2 |
| Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye. |
| 3 |
| Pamenepo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa; |
| 4 |
| anenetsa wakumva mau a Mulungu, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi maso ake openyuka. |
| 5 |
| Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo; zokhalamo zako, Israele! |
| 6 |
| Ziyalika monga zigwa, monga minda m'mphepete mwa nyanja, monga khonje wooka Yehova, monga mikungudza m'mphepete mwa madzi. |
| 7 |
| Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa. |
| 8 |
| Mulungu amtulutsa m'Ejipito; ali nayo mphamvu yonga ya njati; adzawadya amitundu, ndiwo adani ake. Nadzamphwanya mafupa ao, ndi kuwapyoza ndi mivi yake. |
| 9 |
| Anauthama, nagona pansi ngati mkango, ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani? Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe, wotemberereka aliyense wakutemberera iwe. |
| 10 |
| Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano. |
| 11 |
| Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu. |
| 12 |
| Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti, |
| 13 |
| Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine? |
| 14 |
| Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza. |
| 15 |
| Ndipo ananena fanizo lake, nati, Balamu mwana wa Beori anenetsa, ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa; |
| 16 |
| anenetsa wakumva mau a Mulungu, ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba, wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse, wakugwa pansi wopenyuka maso. |
| 17 |
| Ndimuona, koma tsopano ai; ndimpenya, koma si pafupi ai; idzatuluka nyenyezi m'Yakobo, ndi ndodo yachifumu idzauka m'Israele, nidzakantha malire a Mowabu, nidzapasula ana onse a Seti. |
| 18 |
| Ndi Edomu adzakhala akeake, Seiri lomwe lidzakhala lakelake, ndiwo adani ake; koma Israele adzachita zamphamvu. |
| 19 |
| Ndipo wina wotuluka m'Yakobo adzachita ufumu; nadzapasula otsalira m'mudzi. |
| 20 |
| Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse. |
| 21 |
| Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati, kwanu nkokhazikika, wamanga chisa chako m'thanthwe. |
| 22 |
| Koma Kaini adzaonongeka, kufikira Asiriya adzakumanga nsinga. |
| 23 |
| Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ha! Adzakhala ndi moyo ndani pakuchita ichi Mulungu? |
| 24 |
| Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu, ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi, koma iyenso adzaonongeka. |
| 25 |
| Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/numbers/024.mp3
36
24