Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo kunali, utatha mliriwo, Yehova ananena ndi Mose ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, nati, |
| 2 |
| Werenga khamu lonse la ana a Israele, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, monga mwa nyumba za makolo ao, onse akutulukira kunkhondo m'Israele. |
| 3 |
| Pamenepo Mose ndi Eleazara wansembe ananena nao m'zidikha za Mowabu pa Yordani kufupi ku Yeriko, ndi kuti, |
| 4 |
| Awawerenge kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu; monga Yehova anawauza Mose ndi ana a Israele, amene adatuluka m'dziko la Ejipito. |
| 5 |
| Rubeni, ndiye woyamba kubadwa wa Israele; ana amuna a Rubeni ndiwo: Hanoki, ndiye kholo la banja la Ahanoki; Palu, ndiye kholo la banja la Apalu; |
| 6 |
| Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Karimi, ndiye kholo la banja la Akarimi. |
| 7 |
| Iwo ndiwo mabanja a Arubeni; owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zitatu kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. |
| 8 |
| Mwana wamwamuna wa Palu ndiye Eliyabu. |
| 9 |
| Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova; |
| 10 |
| ndipo dziko linayasama pakamwa pake, ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, pakufa msonkhano uja; muja moto unaononga amuna mazana awiri ndi makumi asanu, nakhala iwo chizindikiro. |
| 11 |
| Koma sanafe ana amuna a Kora. |
| 12 |
| Ana amuna a Simeoni monga mwa mabanja ao ndiwo: Nemuwele, ndiye kholo la banja la Anemuwele; Yamini, ndiye kholo la banja la Ayamini; Yakini, ndiye kholo la banja la Ayakini; |
| 13 |
| Zera, ndiye kholo la banja la Azera; Shaulo, ndiye kholo la banja la Ashaulo. |
| 14 |
| Iwo ndiwo mabanja a Asimeoni, zikwi makumi awiri mphambu ziwiri kudza mazana ziwiri. |
| 15 |
| Ana amuna a Gadi monga mwa mabanja ao ndiwo: Zefoni, ndiye kholo la banja la Azefoni; Hagi, ndiye kholo la banja la Ahagi; Suni, ndiye kholo la banja la Suni; |
| 16 |
| Ozini, ndiye kholo la banja la Aozini; Eri, ndiye kholo la banja la Aeri; |
| 17 |
| Arodi, ndiye kholo la banja la Aarodi; Areli, ndiye kholo la banja la Aareli. |
| 18 |
| Iwo ndiwo mabanja a ana a Gadi, monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi anai ndi mazana asanu. |
| 19 |
| Ana amuna a Yuda, ndiwo Eri ndi Onani; ndipo Eri ndi Onani anamwalira m'dziko la Kanani. |
| 20 |
| Ndipo ana a Yuda monga mwa mabanja ao ndiwo: Sela, ndiye kholo la banja la Asela; Perezi, ndiye kholo la banja la Aperezi; Zera, ndiye kholo la banja la Azera. |
| 21 |
| Ndipo ana a Perezi ndiwo: Hezironi, ndiye kholo la banja la Ahezironi; Hamuli, ndiye kholo la banja la Ahamuli. |
| 22 |
| Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu. |
| 23 |
| Ana amuna a Isakara monga mwa mabanja ao ndiwo: Tola, ndiye kholo la banja la Atola; Puva, ndiye kholo la banja la Apuni; |
| 24 |
| Yasubu, ndiye kholo la banja la Ayasubu; Simironi, ndiye kholo la banja la Asimironi. |
| 25 |
| Iwo ndiwo mabanja a Isakara monga mwa owerengedwa ao; zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana atatu. |
| 26 |
| Ana amuna a Zebuloni monga mwa mabanja ao ndiwo: Seredi, ndiye kholo la banja la Aseredi; Eloni, ndiye kholo la banja la Aeloni; Yaleele, ndiye kholo la banja la Ayaleele. |
| 27 |
| Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu. |
| 28 |
| Ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao ndiwo: Manase ndi Efuremu. |
| 29 |
| Ana a Manase ndiwo: Makiri, ndiye kholo la banja la Amakiri; ndipo Makiri anabala Giliyadi; ndiye kholo la banja la Agiliyadi. |
| 30 |
| Ana a Giliyadi ndiwo: Iyezere, ndiye kholo la banja la Aiyezere; Heleki, ndiye kholo la banja la Aheleki; |
| 31 |
| ndi Asiriele, ndiye kholo la banja la Aasiriele; ndi Sekemu, ndiye kholo la banja la Asekemu; |
| 32 |
| ndi Semida, ndiye kholo la banja la Asemida; ndi Hefere, ndiye kholo la banja la Ahefere. |
| 33 |
| Ndipo Zelofehadi mwana wa Hefere analibe ana amuna, koma ana akazi ndiwo; ndipo maina a ana akazi a Tselofekadi ndiwo Mala ndi Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. |
| 34 |
| Iwo ndiwo mabanja ao a Manase; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu mphambu ziwiri kudza mazana asanu ndi awiri. |
| 35 |
| Ana amuna a Efuremu monga mwa mabanja ao ndiwo: Sutela, ndiye kholo la banja la Asutela; Bekere, ndiye kholo la banja la Abekere; Tahani, ndiye kholo la banja la Atahani. |
| 36 |
| Ndipo mwana wamwamuna wa Sutela ndiye Erani, ndiye kholo la banja la Aerani. |
| 37 |
| Iwo ndiwo mabanja a ana a Efuremu monga mwa owerengedwa ao, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu ziwiri kudza mazana asanu. Iwo ndiwo ana amuna a Yosefe monga mwa mabanja ao. |
| 38 |
| Ana amuna a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiwo: Bela, ndiye kholo la banja la Abela; Asibele, ndiye kholo la banja la Aasibele; Ahiramu, ndiye kholo la banja la Aahiramu; |
| 39 |
| Sefufamu ndiye kholo la banja la Asefufamu; Hufamu, ndiye kholo la banja la Ahufamu. |
| 40 |
| Ndipo ana amuna a Bela ndiwo Aridi ndi Naamani; Aridi, ndiye kholo la banja la Aaridi; Naamani, ndiye kholo la banja la Anaamani. |
| 41 |
| Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi. |
| 42 |
| Mwana wamwamuna wa Dani monga mwa mabanja ake ndiye Suhamu, ndiye kholo la banja la Asuhamu. Iwo ndiwo mabanja a Dani monga mwa mabanja ao. |
| 43 |
| Mabanja onse a Asuhamu monga mwa owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu zinai kudza mazana anai. |
| 44 |
| Ana amuna a Asere monga mwa mabanja ao ndiwo: Imina, ndiye kholo la banja la Imina; Isivi, ndiye kholo la banja la Aisivi; Beriya, ndiye kholo la banja la Aberiya. |
| 45 |
| Ana a Beriya ndiwo: Hebere, ndiye kholo la banja la Ahebere; Malikiele, ndiye kholo la banja la Amalikiele. |
| 46 |
| Ndipo dzina la mwana wamkazi wa Asere ndiye Sera. |
| 47 |
| Iwo ndiwo mabanja a ana amuna a Asere monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai. |
| 48 |
| Ana amuna a Nafutali monga mwa mabanja ao ndiwo: Yazeele, ndiye kholo la banja la Ayezeele; Guni, ndiye kholo la banja la Aguni; |
| 49 |
| Yezere, ndiye kholo la banja la Ayezere; Silemu, ndiye kholo la banja la Asilemu. |
| 50 |
| Iwo ndiwo mabanja a Nafutali, monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana anai. |
| 51 |
| Iwo ndiwo owerengedwa ao a ana a Israele, zikwi mazana asanu ndi limodzi mphambu chimodzi kudza mazana asanu ndi awiri mphambu makumi atatu. |
| 52 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, |
| 53 |
| Dziko ligawikire iwowa monga mwa kuwerenga kwa maina, likhale cholowa chao. |
| 54 |
| Ochulukawo, uwachulukitsire cholowa chao; ochepawo uwachepetsere cholowa chao; ampatse yense cholowa chake monga mwa owerengedwa ake. |
| 55 |
| Koma aligawe ndi kuchita maere; cholowa chao chikhale monga mwa maina a mafuko a makolo ao. |
| 56 |
| Agawire ochuluka ndi ochepa cholowa chao monga mwa kuchita maere. |
| 57 |
| Ndipo awa ndi owerengedwa ao a Alevi monga mwa mabanja ao: Geresoni, ndiye kholo la banja la Ageresoni; Kohati, ndiye kholo la banja la Akohati; Merari, ndiye kholo la banja la Amerari. |
| 58 |
| Awa ndi mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, banja la Akora. Ndipo Kohati anabala Amuramu. |
| 59 |
| Ndipo dzina lake la mkazi wake wa Amuramu ndiye Yokebede, mwana wamkazi wa Levi, wobadwira Levi m'Ejipito; ndipo iye anambalira Amuramu, Aroni ndi Mose, ndi Miriyamu mlongo wao. |
| 60 |
| Ndipo Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi Itamara anabadwira Aroni. |
| 61 |
| Koma Nadabu ndi Abihu adafa, muja anabwera nao moto wachilendo pamaso pa Yehova. |
| 62 |
| Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele. |
| 63 |
| Iwo ndiwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eleazara wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'zidikha za Mowabu ku Yordani pafupi pa Yeriko. |
| 64 |
| Koma pakati pao panalibe mmodzi wa iwo amene anawerengedwa ndi Mose ndi Aroni wansembe, amene anawerenga ana a Israele m'chipululu cha Sinai. |
| 65 |
| Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/numbers/026.mp3
36
26