Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Utatha mliri Yehova anati kwa Mose ndi Eliezara mwana wa Aaroni, |
| 2 |
| “Werengani Aisraeli onse mwa mabanja awo, onse a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo omwe angathe kugwira ntchito ya usilikali mʼgulu lankhondo la Israeli.” |
| 3 |
| Kotero mu zigwa za Mowabu pafupi ndi mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, Mose ndi wansembe Eliezara anayankhula nawo kuti, |
| 4 |
| “Werengani amuna a zaka makumi awiri kapena kuposera pamenepo, monga momwe Yehova walamulira Mose.” Aisraeli omwe anachokera ku Igupto ndi awa: |
| 5 |
| Zidzukulu za Rubeni, mwana woyamba wamwamuna wa Israeli, zinali izi: kuchokera mwa Hanoki, fuko la Ahanoki; kuchokera mwa Palu, fuko la Apalu; |
| 6 |
| kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Karimi, fuko la Akarimi. |
| 7 |
| Awa anali mafuko a Rubeni: onse amene anawerengedwa analipo 43,730. |
| 8 |
| Mwana wa Palu anali Eliabu, |
| 9 |
| ndipo ana a Eliabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Datani ndi Abiramu anali gulu la akuluakulu aja amene anawukira Mose ndi Aaroni ndipo analinso mʼgulu la otsatira Kora pamene anawukira Yehova. |
| 10 |
| Nthaka inangʼambika ndi kuwameza pamodzi ndi Kora, kotero kuti gulu lawo linafa pamene moto unapsereza anthu 250 aja, nasanduka chenjezo. |
| 11 |
| Koma ana a Kora sanafe nawo. |
| 12 |
| Zidzukulu za Simeoni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Nemueli, fuko la Anemuele; kuchokera mwa Yamini, fuko la Ayamini; kuchokera mwa Yakini fuko la Ayakini; |
| 13 |
| kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera; kuchokera mwa Sauli, fuko la Asauli. |
| 14 |
| Awa anali mafuko a Simeoni. Iwowa analipo amuna 22,200. |
| 15 |
| Zidzukulu za Gadi mwa mafuko awo ndi izi: kuchokera mwa Zefoni, fuko la Azefoni; kuchokera mwa Hagi, fuko la Ahagi; kuchokera mwa Suni, fuko la Asuni; |
| 16 |
| kuchokera mwa Ozini, fuko la Aozini; kuchokera mwa Eri, fuko la Aeri; |
| 17 |
| kuchokera mwa Arodi, fuko la Aarodi; kuchokera mwa Arieli, fuko la a Areli. |
| 18 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Gadi. Onse amene anawerengedwa analipo 40,500. |
| 19 |
| Eri ndi Onani anali ana aamuna a Yuda, koma anafera mu Kanaani. |
| 20 |
| Zidzukulu za Yuda monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Sela, fuko la Asera; kuchokera mwa Perezi, fuko la Aperezi; kuchokera mwa Zera, mbumba ya Zera. |
| 21 |
| Zidzukulu za Perezi zinali izi: kuchokera mwa Hezironi, fuko la Ahezironi; kuchokera mwa Hamuli, fuko la Ahamuli. |
| 22 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Yuda. Amene anawerenga analipo 76,500. |
| 23 |
| Zidzukulu za Isakara monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Tola, fuko la Atola; kuchokera mwa Puwa, fuko la Apuwa; |
| 24 |
| kuchokera mwa Yasubu, fuko la Ayasubu. Kuchokera mwa Simironi, fuko la Asimironi. |
| 25 |
| Awa ndi amene anali a fuko la Isakara. Amene anawerengedwa analipo 64,300. |
| 26 |
| Zidzukulu za Zebuloni mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Seredi, fuko la Aseredi; kuchokera mwa Eloni, fuko la Aeloni; kuchokera mwa Yahaleeli, fuko la Ayahaleeli. |
| 27 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Zebuloni. Amene anawerengedwa analipo 60,500. |
| 28 |
| Zidzukulu za Yosefe mwa mafuko awo kupyolera mwa Manase ndi Efereimu zinali izi: |
| 29 |
| Zidzukulu za Manase: kuchokera mwa Makiri, fuko la Amakiri (Makiri anali abambo ake a Giliyadi); kuchokera mwa Giliyadi, fuko la Agiliyadi. |
| 30 |
| Izi ndizo zinali zidzukulu za Giliyadi; kuchokera mwa Iyezeri, fuko la Aiyezeri; kuchokera mwa Heleki, fuko la Aheleki; |
| 31 |
| kuchokera mwa Asirieli, fuko la Aasirieli; kuchokera mwa Sekemu, fuko la Asekemu; |
| 32 |
| kuchokera mwa Semida, fuko la Asemida; kuchokera mwa Heferi, fuko la Aheferi. |
| 33 |
| (Zelofehadi mwana wa Heferi analibe ana aamuna koma ana aakazi okha, amene mayina awo anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza.) |
| 34 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Manase. Amene anawerengedwa analipo 52,700. |
| 35 |
| Zidzukulu za Efereimu monga mwa mafuko awo zinali izi; kuchokera mwa Sutela, fuko la Asutela; kuchokera mwa Bekeri, fuko la Abekeri; kuchokera mwa Tahani, fuko la Atahani. |
| 36 |
| Zidzukulu za Sutela zinali izi: kuchokera mwa Erani, fuko la Aerani. |
| 37 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Efereimu. Amene anawerengedwa analipo 32,500. Zimenezi zinali zidzukulu za Yosefe monga mwa mafuko awo. |
| 38 |
| Zidzukulu za Benjamini monga mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Bela, fuko la Abela; kuchokera mwa Asibeli, fuko la Aasibeli; kuchokera mwa Ahiramu, fuko la Ahiramu; |
| 39 |
| kuchokera mwa Sufamu, fuko la Asufamu; kuchokera mwa Hufamu, fuko la Ahufamu; |
| 40 |
| Zidzukulu za Bela kupyolera mwa Aridi ndi Naamani zinali izi: kuchokera mwa Aridi, fuko la Aaridi; kuchokera mwa Naamani, fuko la Anaamani; |
| 41 |
| Awa ndiwo anali mabanja a Benjamini. Amene nawerengedwa analipo 45,600. |
| 42 |
| Zidzukulu za Dani mwa mabanja awo zinali izi: kuchokera mwa Suhamu fuko la Asuhamu. Izi zinali zidzukulu za Dani. |
| 43 |
| Onse a fuko la Asuhamu amene anawerengedwa analipo 64,400. |
| 44 |
| Zidzukulu za Aseri monga mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Imina, fuko la Aimuna; kuchokera mwa Isivi, fuko la Ayisivi; kuchokera mwa Beriya, fuko la Aberiya; |
| 45 |
| ndipo kupyolera mwa zidzukulu za Beriya: kuchokera mwa Heberi, fuko la Aheberi; kuchokera mwa Malikieli, fuko la Amalikieli; |
| 46 |
| (Aseri anali ndi mwana wamkazi dzina lake Sera) |
| 47 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Aseri. Onse amene anawerengedwa analipo 53,400. |
| 48 |
| Zidzukulu za Nafutali mwa mafuko awo zinali izi: kuchokera mwa Yahazeeli, fuko la Ayahazeeli; kuchokera mwa Guni, fuko la Aguni; |
| 49 |
| kuchokera mwa Yezeri, fuko la Ayezeri; kuchokera mwa Silemu, fuko la Asilemu. |
| 50 |
| Awa ndiwo anali mafuko a Nafutali. Onse amene anawerengedwa analipo 45,400. |
| 51 |
| Chiwerengero chonse cha amuna mu Israeli chinalipo 601,730. |
| 52 |
| Yehova anawuza Mose kuti, |
| 53 |
| “Uwagawire dziko anthu awa kuti likhale cholowa chawo molingana ndi chiwerengero cha mayina awo. |
| 54 |
| Gulu lalikulu ulipatse cholowa chachikulu, ndipo lochepa cholowa chocheperapo. Gulu lililonse lilandire cholowa chake molingana ndi chiwerengero cha amene anawerengedwa. |
| 55 |
| Dzikolo uligawe pochita maere. Alandire cholowa chawocho potsata mayina a mafuko a makolo awo. |
| 56 |
| Cholowa chawo uchigawe pakati pa fuko lalikulu ndi lalingʼono mwa maere.” |
| 57 |
| Alevi omwe anawerengedwa monga mwa mafuko awo ndi awa: kuchokera mwa Geresoni, fuko la Ageresoni; kuchokera mwa Kohati, fuko la Akohati; kuchokera mwa Merari, fuko la Amerari. |
| 58 |
| Awanso anali mabanja a Alevi: banja la Alibini, banja la Ahebroni, banja la Amali, banja la Amusi, fuko la Kora banja la Akohati, (Kohati anali abambo a Amramu. |
| 59 |
| Dzina la mkazi wa Amramu linali Yokobedi, mdzukulu wa Levi, yemwe anabadwa mwa Alevi mu Igupto. Yokobedi anaberekera Amramu Aaroni, Mose ndi Miriamu mlongo wawo. |
| 60 |
| Aaroni anali abambo a Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. |
| 61 |
| Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamene anapereka nsembe pamaso pa Yehova ndi moto wachilendo). |
| 62 |
| Alevi onse aamuna a mwezi umodzi kapena kuposera pamenepa analipo 23,000. Iwowo sanawerengedwe pamodzi ndi Aisraeli ena chifukwa sanalandire cholowa pakati pawo. |
| 63 |
| Awa ndi amene anawerengedwa ndi Mose ndi Eliezara wansembe pamene ankawerenga Aisraeli pa zigwa za ku Mowabu mʼmbali mwa Yorodani ku Yeriko. |
| 64 |
| Mwa anthu amenewa panalibe ndi mmodzi yemwe amene anali mʼgulu la Aisraeli omwe Mose ndi wansembe Aaroni anawawerenga mʼchipululu cha Sinai; |
| 65 |
| Chifukwa Yehova anali atawuza Aisraeliwo kuti adzafera ndithu mʼchipululu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/numbers/026.mp3
36
26