Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, |
| 2 |
| Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika. |
| 3 |
| Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza. |
| 4 |
| Mwanawankhosa mmodziyo umpereke m'mawa, ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; |
| 5 |
| ndi limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi limodzi la magawo anai la hini wa mafuta opera. |
| 6 |
| Ndiyo nsembe yopsereza kosalekeza, yoikika kuphiri la Sinai, ichite fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. |
| 7 |
| Ndi nsembe yake yothira ya mwanawankhosa mmodziyo ndiyo limodzi la magawo anai la hini; m'malo opatulika uthirire Yehova nsembe yothira ya chakumwa cholimba. |
| 8 |
| Ndi mwanawankhosa winayo umpereke madzulo; monga nsembe yaufa ya m'mawa, ndi nsembe yothira yake, umpereke; ndiyo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova. |
| 9 |
| Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira; |
| 10 |
| ndiyo nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata lililonse, pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. |
| 11 |
| Ndipo poyamba miyezi yanu muzibwera nayo nsembe yopsereza ya Yehova: ng'ombe zamphongo ziwiri, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi opanda chilema; |
| 12 |
| ndi atatu a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa ng'ombe iliyonse; ndi awiri a magawo khumi a ufa wosalala, ikhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndiwo wa nkhosa yamphongo imodziyo; |
| 13 |
| ndi limodzi la magawo khumi la ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndiwo wa mwanawankhosa yense; ndiyo nsembe yopsereza ya fungo lokoma, nsembe yamoto ya Yehova. |
| 14 |
| Ndipo nsembe zake zothira ndizo: limodzi la magawo khumi la hini wa vinyo ndiwo wa ng'ombe imodzi, ndi limodzi la magawo atatu la hini likhale la nkhosa yamphongo, ndi limodzi la magawo anai a hini likhale la mwanawankhosa; ndiyo nsembe yopsereza ya mwezi uliwonse kunena miyezi yonse ya chaka. |
| 15 |
| Ndi tonde mmodzi, akhale nsembe yauchimo ya Yehova; aikonze pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. |
| 16 |
| Ndipo mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi pali Paska wa Yehova. |
| 17 |
| Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uwu pali zikondwerero; masiku asanu ndi awiri azidya mkate wopanda chotupitsa. |
| 18 |
| Tsiku loyamba pali kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena; |
| 19 |
| koma mubwere nayo nsembe yamoto, nsembe yopsereza ya Yehova; ng'ombe ziwiri zamphongo, ndi nkhosa yamphongo imodzi, ndi anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; akhale kwa inu opanda chilema; |
| 20 |
| ndi nsembe yao ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta; mupereke atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe, ndi awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo; |
| 21 |
| upereke limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi; uzitero ndi anaankhosa asanu ndi awiri; |
| 22 |
| ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo, yakutetezera inu. |
| 23 |
| Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza ya m'mawa, ndiyo ya nsembe yopsereza kosalekeza. |
| 24 |
| Momwemo mupereke chakudya cha nsembe yamoto cha fungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, chakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira. |
| 25 |
| Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri mukhale nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. |
| 26 |
| Momwemonso tsiku la zipatso zoyamba, pobwera nayo nsembe ya ufa watsopano kwa Yehova, m'chikondwerero chanu cha Masabata, muzikhala nako kusonkhana kopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena. |
| 27 |
| Pamenepo muzipereka nsembe yopsereza ya fungo lokoma kwa Yehova; ng'ombe zamphongo ziwiri, nkhosa yamphongo imodzi, anaankhosa asanu ndi awiri a chaka chimodzi; |
| 28 |
| ndi nsembe yake ya efa wa ufa wosalala wosanganiza ndi mafuta, atatu a magawo khumi akhale a ng'ombe imodzi, awiri a magawo khumi akhale a nkhosa yamphongo imodzi, |
| 29 |
| limodzi la magawo khumi likhale la mwanawankhosa mmodzi, momwemo ndi anaankhosa asanu ndi awiri; |
| 30 |
| tonde mmodzi wakutetezera inu. |
| 31 |
| Mupereke izi pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yaufa, zikhale kwa inu zopanda chilema, ndi nsembe zake zothira. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/numbers/028.mp3
36
28