Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Maulendo a ana a Israele amene anatuluka m'dziko la Ejipito monga mwa makamu ao, ndi dzanja la Mose ndi Aroni, ndi awa. |
| 2 |
| Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao. |
| 3 |
| Ndipo anachokera ku Ramsesi mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi woyamba; atachita Paska m'mawa mwake ana a Israele, anatuluka ndi dzanja lokwezeka pamaso pa Aejipito onse, |
| 4 |
| pamene Aejipito analikuika oyamba kubadwa ao onse, amene Yehova adawakantha; Yehova adaweruzanso milungu yao. |
| 5 |
| Ndipo ana a Israele anachokera ku Ramsesi, nayenda namanga ku Sukoti. |
| 6 |
| Nachokera ku Sukoti, nayenda namanga m'Etamu, ndiko ku malekezero a chipululu. |
| 7 |
| Ndipo anachokera ku Etamu, nayenda nabwerera ku Pihahiroti, ndiko kutsogolo kwake kwa Baala-Zefoni; namanga iwo patsogolo pa Migidoli. |
| 8 |
| Ndipo anachokera ku Pihahiroti, naoloka pakati pa nyanja nalowa m'chipululu; nayenda ulendo wa masiku atatu m'chipululu cha Etamu, namanga m'Mara. |
| 9 |
| Ndipo anachokera ku Mara, nayenda nafika ku Elimu, ku Elimu ndiko kuli akasupe khumi ndi awiri a madzi, ndi akanjedza makumi asanu ndi awiri; namanga iwo komweko. |
| 10 |
| Ndipo anachokera ku Elimu, nayenda namanga ku Nyanja Yofiira. |
| 11 |
| Nachokera ku Nyanja Yofiira, nayenda namanga m'chipululu cha Sini. |
| 12 |
| Nachokera ku chipululu cha Sini, nayenda namanga m'Dofika. |
| 13 |
| Nachokera ku Dofika, nayenda namanga m'Alusi. |
| 14 |
| Nachokera ku Alusi, nayenda namanga m'Refidimu; kumeneko kunalibe madzi kuti anthu amwe. |
| 15 |
| Ndipo anachokera ku Refidimu, nayenda namanga m'chipululu cha Sinai. |
| 16 |
| Nachokera ku chipululu cha Sinai, nayenda namanga m'Kibroti-Hatava. |
| 17 |
| Nachokera ku Kibroti-Hatava, nayenda namanga m'Hazeroti. |
| 18 |
| Nachokera ku Hazeroti, nayenda namanga m'Ritima. |
| 19 |
| Nachokera ku Ritima, nayenda namanga m'Rimoni-Perezi. |
| 20 |
| Nachokera ku Rimoni-Perezi, nayenda namanga m'Libina. |
| 21 |
| Nachokera ku Libina, nayenda namanga m'Risa. |
| 22 |
| Nachokera Risa, nayenda namanga m'Kehelata. |
| 23 |
| Nachokera ku Kehelata, nayenda namanga m'phiri la Sefera. |
| 24 |
| Nachokera kuphiri la Sefera, nayenda namanga m'Harada. |
| 25 |
| Nachokera ku Harada, nayenda namanga m'Makeloti. |
| 26 |
| Nachokera ku Makeloti, nayenda namanga m'Tahata. |
| 27 |
| Nachokera ku Tahata, nayenda namanga m'Tera. |
| 28 |
| Nachokera ku Tera, nayenda namanga m'Mitika. |
| 29 |
| Nachokera ku Mitika, nayenda namanga m'Hasimona. |
| 30 |
| Nachokera ku Hasimona, nayenda namanga m'Meseroti. |
| 31 |
| Nachokera ku Meseroti, nayenda namanga m'Bene-Yaakani. |
| 32 |
| Nachokera ku Bene-Yaakani, nayenda namanga m'Hori Hagidigadi. |
| 33 |
| Nachokera ku Hori Hagidigadi, nayenda namanga m'Yotibata. |
| 34 |
| Nachokera ku Yotibata, nayenda namanga m'Aborona. |
| 35 |
| Nachokera ku Aborona, nayenda namanga m'Eziyoni-Gebere. |
| 36 |
| Nachokera ku Eziyoni-Gebere, nayenda namanga m'chipululu cha Zini (ndiko Kadesi). |
| 37 |
| Nachokera ku Kadesi, nayenda namanga m'phiri la Hori, ku malekezero a dziko la Edomu. |
| 38 |
| Ndipo Aroni wansembe anakwera m'phiri la Hori pa mau a Yehova, nafa komweko, atatuluka ana a Israele m'dziko la Ejipito zaka makumi anai, mwezi wachisanu, tsiku loyamba la mwezi. |
| 39 |
| Ndipo Aroni ndiye wa zaka zana limodzi mphambu makumi awiri kudza zitatu pakufa iye m'phiri la Hori. |
| 40 |
| Ndipo Mkanani, mfumu ya Aradi, wakukhala kumwera m'dziko la Kanani, anamva za kudza kwao kwa ana a Israele. |
| 41 |
| Ndipo anachokera kuphiri la Hori, nayenda namanga m'Zalimona. |
| 42 |
| Nachokera ku Zalimona, nayenda namanga m'Punoni. |
| 43 |
| Nachokera ku Punoni, nayenda namanga m'Oboti. |
| 44 |
| Nachokera ku Oboti, nayenda namanga m'Iyeabarimu, m'malire a Mowabu. |
| 45 |
| Nachokera ku Iyimu, nayenda namanga m'Diboni Gadi. |
| 46 |
| Nachokera ku Diboni Gadi, nayenda namanga m'Alimoni-Dibulataimu. |
| 47 |
| Nachokera ku Alimoni-Dibulataimu, nayenda namanga m'mapiri a Abarimu, chakuno cha Nebo. |
| 48 |
| Nachokera ku mapiri a Abarimu, nayenda namanga m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko. |
| 49 |
| Ndipo anamanga pa Yordani, kuyambira ku Beteyesimoti kufikira ku Abele-Sitimu m'zidikha za Mowabu. |
| 50 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose m'zidikha za Mowabu pa Yordani ku Yeriko, nati, |
| 51 |
| Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutaoloka Yordani kulowa m'dziko la Kanani, |
| 52 |
| mupirikitse onse okhala m'dziko pamaso panu, ndi kuononga mafano ao onse a miyala, ndi kuononga mafano ao onse oyenga, ndi kupasula misanje yao yonse; |
| 53 |
| ndipo mulande dziko, ndi kukhala m'mwemo, pakuti ndinakupatsani inu dzikoli likhale lanulanu. |
| 54 |
| Ndipo mulandire dzikoli ndi kuchita maere monga mwa mabanja anu; cholowa chao chichulukire ochulukawo, cholowa chao chichepere ochepawo; kumene maere amgwera munthu, kumeneko nkwake; mulandire cholowa chanu monga mwa mafuko a makolo anu. |
| 55 |
| Koma mukapanda kupirikitsa okhala m'dziko pamaso panu, pamenepo iwo amene muwalola atsale adzakhala ngati zotwikira m'maso mwanu, ndi minga m'mbali zanu, nadzakuvutani m'dziko limene mukhalamo. |
| 56 |
| Ndipo kudzakhala kuti monga ndinayesa kuchitira iwowa, ndidzakuchitirani inu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/numbers/033.mp3
36
33