Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Yehova anawuza Mose kuti, |
| 2 |
| “Lamula Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pamene mulowa mʼdziko la Kanaani, dziko lomwe lidzaperekedwa kwa inu ngati cholowa chanu, lidzakhale ndi malire awa: |
| 3 |
| “ ‘Chigawo cha kummwera kwa dziko lanu chidzayambira ku chipululu cha Zini motsatana ndi malire a Edomu. Kummawa malire anu a kummwera adzayambira kummawa, kumathero a Nyanja ya Mchere. |
| 4 |
| Malirewo adzapita kummwera ndipo adzakwera phiri la Akirabimu mpaka ku Zini. Mathero ake adzakhala kummwera kwa Kadesi-Baranea. Ndipo adzapitenso ku Hazari Adari mpaka kukafika ku Azimoni, |
| 5 |
| kumene malirewo adzakhote kuchokera ku Azimoni mpaka ku khwawa la ku Igupto ndi kukathera ku Nyanja Yayikulu. |
| 6 |
| “ ‘Malire anu a ku madzulo adzakhala ku gombe la Nyanja Yayikulu. Amenewo ndiwo adzakhale malire anu a ku madzulo. |
| 7 |
| “ ‘Malire anu a kumpoto, mzere wake uyambire ku Nyanja Yayikulu mpaka ku phiri la Hori |
| 8 |
| ndi kuchokera ku phiri la Hori mpaka ku Lebo Hamati. Malirewa apite ku Zedadi, |
| 9 |
| ndi kupitirira mpaka ku Ziforoni ndi kukathera ku Hazari-Enani. Awa ndiwo adzakhale malire anu a kumpoto. |
| 10 |
| “ ‘Za malire anu a kummawa, mulembe mzere kuchokera ku Hazari-Enani mpaka kukafika ku Sefamu. |
| 11 |
| Malirewo adzatsikire ku Sefamu mpaka ku Ribila cha kummawa kwa Aini ndi kupitirira mpaka ku matsitso a cha kummawa kwa Nyanja ya Kinereti. |
| 12 |
| Tsono malirewo adzatsika motsatana ndi Yorodani ndi kukathera ku Nyanja ya Mchere. “ ‘Limeneli lidzakhala dziko lanu ndi malire ake mbali zonse.’ ” |
| 13 |
| Ndipo Mose analamula Aisraeli kuti, “Limeneli ndi dziko limene mudzalilandira pochita maere kuti likhale cholowa chanu. Yehova analamula kuti liperekedwe ku mafuko asanu ndi anayi ndi theka, |
| 14 |
| chifukwa mabanja a fuko la Rubeni, fuko la Gadi, ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo. |
| 15 |
| Mafuko awiriwa pamodzi ndi theka la fuko la Manase analandiriratu cholowa chawo patsidya pa mtsinje wa Yorodani ku Yeriko cha kummawa kotulukira dzuwa.” |
| 16 |
| Yehova anawuza Mose kuti, |
| 17 |
| “Awa ndi mayina a anthu amene adzakugawireni dzikoli kuti likhale cholowa chanu: wansembe Eliezara ndi Yoswa mwana wa Nuni. |
| 18 |
| Musankhe mtsogoleri mmodzi kuchokera ku fuko lililonse kuti athandize kugawa dzikolo. |
| 19 |
| Mayina awo ndi awa: Kalebe mwana wa Yefune, wochokera ku fuko la Yuda, |
| 20 |
| Semueli mwana wa Amihudi, wochokera ku fuko la Simeoni; |
| 21 |
| Elidadi mwana wa Kisiloni, wochokera ku fuko la Benjamini; |
| 22 |
| Buki mwana wa Yogili, mtsogoleri wochokera ku fuko la Dani; |
| 23 |
| Hanieli mwana wa Efodi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Manase, mwana wa Yosefe; |
| 24 |
| Kemueli mwana wa Sifitani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Efereimu, mwana wa Yosefe. |
| 25 |
| Elizafani mwana wa Parinaki, mtsogoleri wochokera ku fuko la Zebuloni; |
| 26 |
| Palitieli mwana wa Azani, mtsogoleri wochokera ku fuko la Isakara, |
| 27 |
| Ahihudi mwana wa Selomi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Aseri; |
| 28 |
| Pedaheli mwana wa Amihudi, mtsogoleri wochokera ku fuko la Nafutali.” |
| 29 |
| Awa ndiwo mayina a anthu amene Yehova analamula kuti agawe cholowa cha Aisraeli mʼdziko la Kanaani. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/numbers/034.mp3
36
34