Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, |
| 2 |
| Nena kwa Aroni, nuti naye, Pamene uyatsa nyalizo, nyali zisanu ndi ziwirizo ziwale pandunji pake pa choikapo nyalicho. |
| 3 |
| Ndipo Aroni anachita chotero; anayatsa nyalizo kuti ziwale pandunji pake pa choikapo nyali, monga Yehova adauza Mose. |
| 4 |
| Ndipo mapangidwe ake a choikapo nyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikapo nyali. |
| 5 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, |
| 6 |
| Uwatenge Alevi pakati pa ana a Israele, nuwayeretse. |
| 7 |
| Ndipo utere nao kuwayeretsa: uwawaze madzi akuchotsa zoipa, ndipo apititse lumo pa thupi lao lonse, natsuke zovala zao, nadziyeretse. |
| 8 |
| Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosanganiza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo. |
| 9 |
| Ndipo ubwere nao Alevi pakhomo pa chihema chokomanako; nuwasonkhanitse khamu lonse la ana a Israele; |
| 10 |
| nubwere nao Alevi pamaso pa Yehova; ndi ana a Israele aike manja ao pa Alevi; |
| 11 |
| ndi Aroni apereke Alevi ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, yochokera kwa ana a Israele, kuti akhale akuchita ntchito ya Yehova, |
| 12 |
| Ndipo Alevi aike manja ao pa mitu ya ng'ombezo; pamenepo ukonze imodzi ikhale nsembe yauchimo, ndi inzake, nsembe yopsereza za Yehova, kuchita chotetezera Alevi. |
| 13 |
| Ndipo uimike Alevi pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula kwa Yehova. |
| 14 |
| Momwemo upatule Alevi mwa ana a Israele; kuti Alevi akhale anga. |
| 15 |
| Ndipo atatero alowe Alevi kuchita ntchito ya chihema chokomanako; ndipo uwayeretse, ndi kuwapereka ngati nsembe yoweyula. |
| 16 |
| Pakuti aperekedwa konse kwa Ine ochokera mwa ana a Israele; ndadzitengera iwo m'malo mwa onse akutsegula m'mimba, ndiwo oyamba kubadwa a ana a Israele. |
| 17 |
| Pakuti oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele ndi anga, mwa anthu ndi zoweta; tsiku lija ndinakantha oyamba kubadwa onse m'dziko la Ejipito, ndinadzipatulira iwo akhale anga. |
| 18 |
| Ndipo ndatenga Alevi m'malo mwa oyamba kubadwa onse mwa ana a Israele. |
| 19 |
| Ndipo ndapereka Alevi akhale mphatso ya kwa Aroni ndi ana ake amuna yochokera mwa ana a Israele, kuchita ntchito ya ana a Israele, m'chihema chokomanako ndi kuchita chotetezera ana a Israele; kuti pasakhale mliri pakati pa ana a Israele, pakuyandikiza ana a Israele ku malo opatulika. |
| 20 |
| Ndipo Mose ndi Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele anachitira Alevi monga mwa zonse Yehova adauza Mose kunena za Alevi; momwemo ana a Israele anawachitira. |
| 21 |
| Ndipo Alevi anadziyeretsa, natsuka zovala zao; ndi Aroni anawapereka ngati nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndi Aroni anawachitira chotetezera kuwayeretsa. |
| 22 |
| Ndipo atatero, Alevi analowa kuchita ntchito yao m'chihema chokomanako pamaso pa Aroni, ndi pamaso pa ana ake amuna; monga Yehova anauza Mose kunena za Alevi, momwemo anawachitira. |
| 23 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati, |
| 24 |
| Ichi ndi cha Alevi: kuyambira ali wa zaka makumi awiri ndi zisanu ndi mphambu azilowa kutumikira utumikiwu mu ntchito ya chihema chokomanako; |
| 25 |
| ndipo kuyambira zaka makumi asanu azileka kutumikira utumikiwu, osachitanso ntchitoyi; |
| 26 |
| koma atumikire pamodzi ndi abale ao m'chihema chokomanako, kusunga udikirowo, koma osagwira ntchito. Utere nao Alevi kunena za udikiro wao. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/numbers/008.mp3
36
8