Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'chipululu cha Yudeya, |
| 2 |
| nanena, Tembenukani mitima; chifukwa Ufumu wa Kumwamba wayandikira. |
| 3 |
| Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake. |
| 4 |
| Ndipo Yohane yekhayo anali nacho chovala chake cha ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m'chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wa kuthengo. |
| 5 |
| Pamenepo panamtulukira iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani; |
| 6 |
| nabatizidwa ndi iye mu mtsinjewo wa Yordani, alikuwulula machimo ao. |
| 7 |
| Ndipo iye pakuona ambiri a Afarisi ndi a Asaduki akudza ku ubatizo wake, anati kwa iwo, Obadwa a njoka inu, ndani anakulangizani kuthawa mkwiyo ulinkudza? |
| 8 |
| Onetsani inu zipatso zakuyenera kutembenuka mtima: |
| 9 |
| ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye Abrahamu; pakuti ndinena kwa inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana. |
| 10 |
| Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto. |
| 11 |
| Inetu ndikubatizani inu ndi madzi kuloza ku kutembenuka mtima; koma Iye wakudza pambuyo panga, ali wakundiposa mphamvu, amene sindiyenera kunyamula nsapato zake: Iyeyu adzakubatizani inu ndi Mzimu Woyera ndi moto: |
| 12 |
| chouluzira chake chili m'dzanja lake, ndipo adzayeretsa padwale pake; ndipo adzasonkhanitsa tirigu wake m'nkhokwe, koma mankhusu adzatentha ndi moto wosazima. |
| 13 |
| Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordani kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi iye. |
| 14 |
| Koma Yohane anati amkanize, nanena, Ndiyenera ine kubatizidwa ndi Inu, ndipo Inu mudza kwa ine kodi? |
| 15 |
| Koma Yesu anayankha, nati kwa iye, Balola tsopano: pakuti kuyenera ife kukwaniritsa chilungamo chonse motero. Pamenepo anamlola Iye. |
| 16 |
| Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; |
| 17 |
| ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/matthew/003.mp3
28
3