Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. |
| 2 |
| Ndipo pamene Iye analibe kudya masiku makumi anai usana ndi usiku, pambuyo pake anamva njala. |
| 3 |
| Ndipo woyesayo anafika nanena kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tauzani kuti miyala iyi isanduke mikate. |
| 4 |
| Koma Iye anayankha nati, Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mau onse akutuluka m'kamwa mwa Mulungu. |
| 5 |
| Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi, |
| 6 |
| nanena naye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, mudzigwetse nokha pansi: pakuti kwalembedwa, kuti, Adzalamula angelo ake za iwe, ndipo pa manja ao adzakunyamula iwe, ungagunde konse phazi lako pamwala. |
| 7 |
| Yesu ananena naye, Ndiponso kwalembedwa, Usamuyese Ambuye Mulungu wako. |
| 8 |
| Pomwepo mdierekezi anamuka naye kuphiri lalitali, namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wao; |
| 9 |
| nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine. |
| 10 |
| Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira. |
| 11 |
| Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye. |
| 12 |
| Ndipo pamene Yesu anamva kuti anampereka Yohane, anamuka kulowa ku Galileya; |
| 13 |
| ndipo anachoka ku Nazarete nadza nakhalitsa Iye m'Kapernao wa pambali pa nyanja, m'malire a Zebuloni ndi Nafutali: |
| 14 |
| kuti chikachitidwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, |
| 15 |
| Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, njira ya kunyanja, kutsidya lija la Yordani, Galileya la anthu akunja, |
| 16 |
| anthu akukhala mumdima adaona kuwala kwakukulu, ndi kwa iwo okhala m'malo a mthunzi wa imfa, kuwala kunatulukira iwo. |
| 17 |
| Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira. |
| 18 |
| Ndipo pamene Yesu analikuyenda m'mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wonenedwa Petro, ndi Andrea, mbale wake, analikuponya khoka m'nyanja; popeza anali asodzi a nsomba. |
| 19 |
| Ndipo Iye ananena nao, Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu. |
| 20 |
| Ndipo iwo anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye. |
| 21 |
| Ndipo popitirirapo Iye anaona abale ena awiri, Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, m'ngalawa, pamodzi ndi Zebedeo atate wao, analikusoka makoka ao; ndipo anaitana iwo. |
| 22 |
| Ndipo anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wao, namtsata Iye. |
| 23 |
| Ndipo Yesu anayendayenda m'Galileya monse, analikuphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu, nachiritsa nthenda zonse ndi kudwala konse mwa anthu. |
| 24 |
| Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa. |
| 25 |
| Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/matthew/004.mp3
28
4