Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo m'mene Iye anaona makamu, anakwera m'phiri; ndipo m'mene Iye anakhala pansi, anadza kwa Iye ophunzira ake; |
| 2 |
| ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati: |
| 3 |
| Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. |
| 4 |
| Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa. |
| 5 |
| Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi. |
| 6 |
| Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta. |
| 7 |
| Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo. |
| 8 |
| Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu. |
| 9 |
| Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. |
| 10 |
| Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. |
| 11 |
| Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine. |
| 12 |
| Sekerani, sangalalani: chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu m'Mwamba: pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu. |
| 13 |
| Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu. |
| 14 |
| Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika. |
| 15 |
| Kapena sayatsa nyali, ndi kuivundikira m'mbiya, koma aiika iyo pa choikapo chake; ndipo iunikira onse ali m'nyumbamo. |
| 16 |
| Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba. |
| 17 |
| Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa. |
| 18 |
| Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse. |
| 19 |
| Chifukwa chake yense wakumasula limodzi la malamulo amenewa ang'onong'ono, nadzaphunzitsa anthu chomwecho, adzatchulidwa wamng'onong'ono mu Ufumu wa Kumwamba; koma yense wakuchita ndi kuphunzitsa awa, iyeyu adzatchulidwa wamkulu mu Ufumu wa Kumwamba. |
| 20 |
| Pakuti ndinena ndi inu, ngati chilungamo chanu sichichuluka choposa cha alembi ndi Afarisi, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba. |
| 21 |
| Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: |
| 22 |
| koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto. |
| 23 |
| Chifukwa chake ngati ulikupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, |
| 24 |
| usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako. |
| 25 |
| Fulumira kuyanjana ndi mnzako wamlandu, pamene uli naye panjira; kapena mnzako wamlandu angakupereke iwe kwa woweruza mlandu, ndi woweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, nuponyedwe iwe m'nyumba yandende. |
| 26 |
| Indetu ndinena ndi iwe, sudzatulukamo konse, koma utalipa kakobiri kakumaliza ndiko. |
| 27 |
| Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; |
| 28 |
| koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake. |
| 29 |
| Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m'Gehena. |
| 30 |
| Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena. |
| 31 |
| Kunanenedwanso, Yense wakuchotsa mkazi wake ampatse iye chilekaniro: |
| 32 |
| koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo. |
| 33 |
| Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako: |
| 34 |
| koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; |
| 35 |
| kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu. |
| 36 |
| Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. |
| 37 |
| Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo. |
| 38 |
| Munamva kuti kunanenedwa, Diso kulipa diso, ndi dzino kulipa dzino: |
| 39 |
| koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso. |
| 40 |
| Ndipo kwa iye wofuna kupita nawe kumlandu ndi kutenga malaya ako, umlolezenso chofunda chako. |
| 41 |
| Ndipo amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziwiri. |
| 42 |
| Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere. |
| 43 |
| Munamva kuti kunanenedwa, Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako: |
| 44 |
| koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; |
| 45 |
| kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama. |
| 46 |
| Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho? |
| 47 |
| Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho? |
| 48 |
| Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/matthew/005.mp3
28
5