Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo pakutsika pake paphiripo, inamtsata mipingo yambiri ya anthu. |
| 2 |
| Ndipo onani, wakhate anadza namgwadira Iye, nanena, Ambuye ngati mufuna mungathe kundikonza. |
| 3 |
| Ndipo Yesu anatambalitsa dzanja lake, namkhudza iye, nati, Ndifuna; takonzedwa. Ndipo pomwepo khate lake linachoka. |
| 4 |
| Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo. |
| 5 |
| Ndipo m'mene Iye analowa m'Kapernao anadza kwa Iye kenturiyo, nampemba Iye, |
| 6 |
| nati, Ambuye, mnyamata wanga ali gone m'nyumba wodwala manjenje, wozunzidwa koopsa. |
| 7 |
| Ndipo Yesu ananena naye, Ndifika Ine, ndidzamchiritsa iye. |
| 8 |
| Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa chindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga. |
| 9 |
| Pakuti inenso ndili munthu wakumvera ulamuliro, ndili nao asilikali akundimvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndi kwa kapolo wanga, Chita ichi, nachita. |
| 10 |
| Ndipo pakumva ichi, Yesu anazizwa, nati kwa iwo akumtsata, Indetu ndinena kwa inu, ngakhale mwa Israele, sindinapeza chikhulupiriro chotere. |
| 11 |
| Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba; |
| 12 |
| koma anawo a Ufumu adzatayidwa kumdima wakunja; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano. |
| 13 |
| Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo. |
| 14 |
| Ndipo pofika Yesu kunyumba ya Petro, anaona mpongozi wake ali gone, alikudwala malungo. |
| 15 |
| Ndipo anamkhudza dzanja lake, ndipo malungo anamleka mkaziyo; ndipo anauka, namtumikira Iye. |
| 16 |
| Ndipo pakudza madzulo, anabwera nao kwa Iye anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda; ndipo Iye anatulutsa mizimuyo ndi mau, nachiritsa akudwala onse; |
| 17 |
| kotero kuti chikwaniridwe chonenedwa ndi Yesaya mneneri, kuti, Iye yekha anatenga zofooka zathu, nanyamula nthenda zathu. |
| 18 |
| Ndipo Yesu, poona makamu ambiri a anthu akumzungulira Iye, analamulira ophunzira amuke kutsidya lina. |
| 19 |
| Ndipo anadza munthu mlembi, nati kwa Iye, Mphunzitsi, ndidzakutsatani Inu kulikonse mumukako. |
| 20 |
| Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake. |
| 21 |
| Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga. |
| 22 |
| Koma Yesu ananena kwa iye, Tsata Ine, nuleke akufa aike akufa ao. |
| 23 |
| Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye. |
| 24 |
| Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo. |
| 25 |
| Ndipo iwo anadza, namuutsa Iye, nanena, Ambuye, tipulumutseni, tilikutayika. |
| 26 |
| Ndipo ananena Iye kwa iwo, Muli amantha bwanji, okhulupirira pang'ono inu? Pomwepo Iye anauka, nadzudzula mphepo ndi nyanja, ndipo panagwa bata lalikulu. |
| 27 |
| Ndipo anazizwa anthuwo nanena, Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye? |
| 28 |
| Ndipo pofika Iye kutsidya lina, kudziko la Agadara, anakomana naye awiri ogwidwa ndi ziwanda, akutuluka kumanda, aukali ndithu, kotero kuti sangathe kupitapo munthu pa njira imeneyo. |
| 29 |
| Ndipo onani, anafuula nati, Tili nanu chiyani, Inu Mwana wa Mulungu? Mwadza kuno kodi kutizunza ife, nthawi yake siinafike? |
| 30 |
| Ndipo panali patali ndi iwo gulu la nkhumba zambiri zilinkudya. |
| 31 |
| Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. |
| 32 |
| Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi. |
| 33 |
| Koma akuziweta anathawa, namuka kumidzi, nauza zonse, ndi zakuti zao za aziwanda aja. |
| 34 |
| Ndipo onani, mudzi wonse unatulukira kukakumana naye Yesu, ndipo m'mene anamuona Iye, anampempha kuti achoke m'malire ao. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/matthew/008.mp3
28
8