Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumudzi kwao. |
| 2 |
| Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa. |
| 3 |
| Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano. |
| 4 |
| Ndipo Yesu, pozindikira maganizo ao, anati, Chifukwa chanji mulinkuganizira zoipa m'mitima yanu? |
| 5 |
| Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende? |
| 6 |
| Koma kuti mudziwe kuti ali nazo mphamvu Mwana wa Munthu pansi pano za kukhululukira machimo (pomwepo ananena kwa wodwalayo), Tanyamuka, nutenge mphasa yako, numuke kunyumba kwako. |
| 7 |
| Ndipo ananyamuka, napita kunyumba kwake. |
| 8 |
| Ndipo m'mene anthu a makamu anachiona, anaopa, nalemekeza Mulungu, wakupatsa anthu mphamvu yotere. |
| 9 |
| Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata. |
| 10 |
| Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. |
| 11 |
| Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa? |
| 12 |
| Ndipo m'mene Yesu anamva anati, Olimba safuna sing'anga ai, koma odwala. |
| 13 |
| Koma mukani muphunzire nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, si nsembe ai; pakuti sindinadza kudzaitana olungama, koma ochimwa. |
| 14 |
| Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala? |
| 15 |
| Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya. |
| 16 |
| Ndipo kulibe munthu aphathika chigamba cha nsalu yaiwisi pa chofunda chakale; pakuti chigamba chake chizomoka kuchofundacho, ndipo chichita chiboo chachikulu. |
| 17 |
| Kapena samathira vinyo watsopano m'matumba akale; akatero, matumba aphulika, ndi vinyo atayika, ndi matumba aonongeka; koma athira vinyo watsopano m'matumba atsopano, ndi zonse ziwiri zisungika. |
| 18 |
| M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo. |
| 19 |
| Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe. |
| 20 |
| Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake; |
| 21 |
| pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira. |
| 22 |
| Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo. |
| 23 |
| Ndipo Yesu polowa m'nyumba yake ya mkuluyo, ndi poona oimba zitoliro ndi khamu la anthu obuma, |
| 24 |
| ananena, Tulukani, pakuti kabuthuko sikanafa koma kali m'tulo. Ndipo anamseka Iye pwepwete. |
| 25 |
| Koma pamene khamulo linatulutsidwa, Iye analowamo, nagwira dzanja lake; ndipo kabuthuko kadauka. |
| 26 |
| Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo. |
| 27 |
| Ndipo popita Yesu kuchokera kumeneko, anamtsata Iye anthu awiri akhungu, ofuula ndi kuti, Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide. |
| 28 |
| Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye. |
| 29 |
| Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu. |
| 30 |
| Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense. |
| 31 |
| Koma iwo anatulukamo, nabukitsa mbiri yake m'dziko lonselo. |
| 32 |
| Ndipo pamene iwo analikutuluka, onani, anabwera naye kwa Iye munthu wosalankhula, wogwidwa ndi chiwanda. |
| 33 |
| Ndipo m'mene chinatulutsidwa chiwandacho, wosalankhulayo analankhula, ndipo makamu a anthu anazizwa, nanena, Kale lonse sichinaoneke chomwecho mwa Israele. |
| 34 |
| Koma Afarisi analinkunena, Atulutsa ziwanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziwanda. |
| 35 |
| Ndipo Yesu anayendayenda m'mizinda yonse ndi m'midzi, namaphunzitsa m'masunagoge mwao, nalalikira Uthenga Wabwino wa Ufumuwo, nachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse. |
| 36 |
| Koma Iye, poona makamuwo, anagwidwa m'mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa. |
| 37 |
| Pomwepo ananena kwa ophunzira ake, Zotuta zichulukadi koma antchito ali owerengeka. |
| 38 |
| Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/matthew/009.mp3
28
9