Buku Loyera
|
| 1 |
| Kudangotsala masiku aŵiri kuti chifike chikondwerero cha Paska ndi chikondwerero cha masiku odya buledi wosafufumitsa. Akulu a ansembe ndi aphunzitsi a Malamulo ankafunafuna njira yoti amgwirire Yesu mochenjera, nkumupha. |
| 2 |
| Koma ankati, “Zimenezi tisadzachite pa nthaŵi ya chikondwerero ai, pangadzachitike chipolowe pakati pa anthu.” |
| 3 |
| Tsiku lina Yesu anali ku Betaniya, m'nyumba ya Simoni wotchedwa Wakhate. Pamene ankadya, kudafika mai wina atatenga nsupa yagalasi ya mafuta enieni onunkhira, amtengowapatali, a mtundu wa narido. Maiyo adaphwanya nsupa ija, nayamba kuthira mafutawo pamutu pa Yesu. |
| 4 |
| Anthu ena pamenepo adaipidwa nazo nanena kuti, “Chifukwa chiyani kuŵasakaza chotere mafuta onunkhiraŵa? |
| 5 |
| Ndithu mafuta ameneŵa akadatha kuŵagulitsa, pa mtengo wopitirira ndalama zasiliva mazana atatu, kenaka ndalamazo nkukapatsa anthu osauka?” Choncho anthuwo adamupsera mtima mai uja. |
| 6 |
| Koma Yesu adati, “Mlekeni maiyu, mukumuvutiranji kodi? Zimenetu wandichitira iyeyuzi nzabwino kwambiri. |
| 7 |
| Anthu osauka muli nawo nthaŵi zonse, kotero kuti pamene mufuna kuŵachitira zachifundo, mungathe kuŵachitira. Koma Ine simudzakhala nane nthaŵi zonse. |
| 8 |
| Iyeyu wachita zimene akadatha kuchita. Wadzozeratu thupi langa ndi mafuta onunkhira, kuti alikonzeretu lisanaikidwe m'manda. |
| 9 |
| Ndithu ndikunenetsa kuti kulikonse kumene anthu azikalalika Uthenga Wabwino pa dziko lonse lapansi, azidzafotokozanso zimene maiyu wachita, kuti anthu azidzamkumbukira.” |
| 10 |
| Pambuyo pake Yudasi Iskariote, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja, adapita kwa akulu a ansembe kuti akapereke Yesu kwa iwo. |
| 11 |
| Pamene iwo adamva zimenezi adakondwa, ndipo adamlonjeza kuti adzampatsa ndalama. Iyeyo tsono adayamba kufunafuna mpata womuperekera kwa iwo. |
| 12 |
| Pa tsiku loyamba la masiku a buledi wosafufumitsa, tsiku lomwe anthu ankapha mwanawankhosa wochitira phwando la Paska, ophunzira a Yesu adamufunsa kuti, “Kodi tikakukonzereni kuti malo okadyerako phwando la Paska?” |
| 13 |
| Yesu adatuma aŵiri mwa ophunzira ake, naŵauza kuti, “Pitani m'mudzimu. Mukumana ndi munthu wamwamuna atasenza mtsuko wa madzi. Mukamtsatire. |
| 14 |
| Kunyumba kumene ati akaloŵe, mukauze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa kuti, kodi nchiti chipinda cha alendo choti Iwowo adzadyeremo phwando la Paska ndi ophunzira ao?’ |
| 15 |
| Iyeyo akakuwonetsani chipinda chachikulu cham'mwamba, momwe akonzamo zonse zofunikira. M'menemo mukatikonzere chakudya.” |
| 16 |
| Ophunzira aja adanyamuka naloŵa mumzindamo. Adachipezadi monga momwe Yesu adaaŵauzira, ndipo adakonza za phwando la Paska. |
| 17 |
| Kutada, Yesu adabwera ndi ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja. |
| 18 |
| Onse atakhala pansi nkumadya, Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti wina mwa inu, mnzanga wodya nane, andipereka kwa adani anga.” |
| 19 |
| Ophunzirawo adamva chisoni, nayamba mmodzimmodzi kumufunsa kuti, “Monga nkukhala ine?” |
| 20 |
| Yesu adaŵayankha kuti, “Ndi wina ndithu mwa khumi ndi aŵirinu, yemwe akusunsa mkate m'mbalemu pamodzi ndi ine. |
| 21 |
| Mwana wa Munthu akukaphedwadi, monga momwe Malembo akunenera za Iye. Komabe ali ndi tsoka munthu amene akukapereka Mwana wa Munthuyo. Kukadakhala bwino koposa kwa munthu ameneyo, akadapanda kubadwa.” |
| 22 |
| Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.” |
| 23 |
| Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse. |
| 24 |
| Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka. |
| 25 |
| Kunena zoona, sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.” |
| 26 |
| Tsono ataimba nyimbo yotamanda Mulungu, onse adatuluka nkumapita ku Phiri la Olivi. |
| 27 |
| Pambuyo pake Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa zidzangoti balala.’ |
| 28 |
| Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola ndine kupita ku Galileya.” |
| 29 |
| Petro adati, “Ngakhale onse akhumudwe nkukusiyani, ine ndekha ai.” |
| 30 |
| Yesu adamuuza kuti, “Ndithu ndikunenetsa kuti lero lomwe lino usiku womwe uno, tambala asanalire kachiŵiri, ukhala utandikana katatu kuti Ine sundidziŵa.” |
| 31 |
| Apo Petro adanenetsanso kuti, “Ngakhale atati andiphere nanu kumodzi, ine sindingakukaneni konse kuti sindikudziŵani.” Ophunzira ena onse aja nawonso adanena chimodzimodzi. |
| 32 |
| Yesu adapita ndi ophunzira ake aja ku malo ena, otchedwa Getsemani. Tsono adauza ophunzirawo kuti, “Inu bakhalani pano, Ine ndikukapemphera.” |
| 33 |
| Adatengako Petro, Yakobe ndi Yohane. Yesu adayamba kugwidwa ndi chisoni ndi kuvutika mu mtima. |
| 34 |
| Adaŵauza kuti, “Mumtima mwanga muli chisoni chachikulu chofa nacho. Inu khalani pompano, koma mukhale masotu.” |
| 35 |
| Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa pansi, nkuyamba kupemphera. Adati, “Ngati nkotheka nthaŵi yoopsa ino indipitirire.” |
| 36 |
| Adanenanso kuti, “Abba, Atate, mungathe kuchita chilichonse. Mundichotsere chikho cha masautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.” |
| 37 |
| Atatero adabwerera kwa ophunzira aja, naŵapeza ali m'tulo. Tsono adafunsa Petro kuti, “Simoni, uli m'tulo kodi iwe? Mongadi walephera kukhala maso ndi kanthaŵi kochepa komwe? |
| 38 |
| Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.” |
| 39 |
| Adachokanso nakapemphera ndi mau omwe aja. |
| 40 |
| Pamene adabwerakonso, adaŵapeza ali m'tulo, chifukwa zikope zao zinkalemera ndi tulo. Choncho iwowo adasoŵa choyankha. |
| 41 |
| Pamene adabwerako kachitatu, adati, “Kodi monga mukugonabe ndi kupumula? Basi tsopano. Nthaŵi ija yafika, Mwana wa Munthu akuperekedwa kwa anthu ochimwa. |
| 42 |
| Dzukani, tiyeni tizipita. Suuyu wodzandipereka uja, wafika.” |
| 43 |
| Yesu akulankhula choncho, nthaŵi yomweyo wafika Yudasi, mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja. Adaabwera ndi khamu la anthu atatenga malupanga ndi zibonga. Anthuwo adaaŵatuma ndi akulu a ansembe, aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. |
| 44 |
| Wodzampereka uja anali ataŵauza chizindikiro kuti, “Yemwe ndikamumpsompsoneyo, ndi ameneyo. Mukamgwire nkupita naye, osamtaya.” |
| 45 |
| Pamene Yudasi adabwera, adadzangofikira pa Yesu, nkunena kuti, “Aphunzitsi!” Atatero adamumpsompsona. |
| 46 |
| Apo anthu aja adamugwira Yesu. |
| 47 |
| Koma wina mwa ophunzira amene anali naye pamenepo, adasolola lupanga lake, natema wantchito wa mkulu wa ansembe onse, mpaka kumusenga khutu. |
| 48 |
| Tsono Yesu adaŵafunsa anthu aja kuti, “Bwanji mwachita kunditengera malupanga ndi zibonga, ngati kuti ndine chigaŵenga? |
| 49 |
| Tsiku ndi tsiku ndidaali nanu m'Nyumba ya Mulungu ndikuphunzitsa, inuyo osandigwira. Koma izi zatere kuti zipherezere zomwe Malembo adanena.” |
| 50 |
| Pamenepo ophunzira ake onse aja adathaŵa, kumsiya yekha. |
| 51 |
| Mnyamata wina ankatsatira Yesu, atangofundira nsalu yokha, opanda chovala china. Anthu aja adaati amgwire, |
| 52 |
| koma iye adaikolopola nsalu ija, nkuthaŵa ali maliseche. |
| 53 |
| Tsono anthu aja adapita naye Yesu kwa mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana onse akulu a ansembe, akulu a Ayuda, ndi aphunzitsi a Malamulo. |
| 54 |
| Petro ankamutsatira Yesu chapatali, mpaka ku bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe uja. Adakhala pansi pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, nkumaotha nao moto. |
| 55 |
| Akulu a ansembe aja ndi onse a m'Bwalo Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni woneneza Yesu kuti amuphe, koma osaupeza. |
| 56 |
| Ambiritu ankamuneneza zabodza, koma umboni wao sunkagwirizana. |
| 57 |
| Ena adaimirira nayamba kumneneza zabodza. |
| 58 |
| Adati, “Munthu uyu ife tidamumva akunena kuti, ‘Ine ndidzapasula Nyumba ya Mulunguyi, yomangidwa ndi anthu chabe, ndipo patapita masiku atatu ndidzamanga ina yosamangidwa ndi anthu.’ ” |
| 59 |
| Koma ngakhale aponso zokamba zaozo sizinali zogwirizana. |
| 60 |
| Tsono mkulu wa ansembe onse adaimirira pamaso pao, nafunsa Yesu kuti, “Kodi ulibe poyankha? Nzotani zimene anthuŵa akukunenezazi?” |
| 61 |
| Yesu adangokhala chete, osayankha kanthu. Pamenepo mkulu wa ansembe uja adafunsanso kuti, “Kodi ndiwedi Mpulumutsi wolonjezedwa uja, Mwana wa Mulungu Wolemekezeka?” |
| 62 |
| Yesu adayankha kuti, “Inde, ndinedi. Ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala ku dzanja lamanja la Mulungu wamphamvuzonse. Mudzamuwona akubwera pa mitambo.” |
| 63 |
| Apo mkulu wa ansembe uja adang'amba zovala zake, nati, “Kodi pamenepa tikusoŵanso mboni zina? |
| 64 |
| Mwadzimvera nokha kunyoza Mulungu koopsaku. Tsono mukuganiza bwanji?” Onse adagamula kuti ayenera kuphedwa. |
| 65 |
| Ena adayamba kumthira malovu, namuphimba m'maso nkumamuwomba makofi, namanena kuti, “Lotatu, wakumenya ndani?” Alonda aja nawonso adayamba kummenya. |
| 66 |
| Petro anali kunsi pa bwalo. Mtsikana wina, wantchito wa mkulu wa ansembe onse, adafika pomwepo. |
| 67 |
| Ataona Petro akuwotha moto, adamuyang'anitsitsa, nati, “Inunsotu munali ndi Yesu wa ku Nazareteyu.” |
| 68 |
| Koma Petro adakana, adati, “Zimenezo ine sindikuzidziŵa, sindikuzimvetsa konse.” Ndipo adatuluka kumapita cha ku chipata. Pamenepo tambala adalira. |
| 69 |
| Koma mtsikana uja adamuwona, nayambanso kuuza amene anali pamenepo kuti, “Akulu ameneŵa anali m'gulu lomweli.” |
| 70 |
| Koma Petro adakananso. Patangopita kanthaŵi, anthu amene adaali pamenepo adamuuza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli. Kodi kwanu si ku Galileya iwe?” |
| 71 |
| Koma Petro adayamba kudzitemberera nkumalumbira kuti, “Mtheradi, munthu amene mukunenayu ine sindimdziŵa.” |
| 72 |
| Nthaŵi yomweyo tambala adalira kachiŵiri. Tsono Petro adakumbukira mau aja a Yesu akuti, “Tambala asanalire kaŵiri, ukhala utakana katatu kuti sundidziŵa.” Pomwepo Petro adayamba kulira misozi. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/mark/014.mp3
16
14