Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato. |
| 2 |
| Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.” |
| 3 |
| Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri. |
| 4 |
| Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.” |
| 5 |
| Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa. |
| 6 |
| Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha. |
| 7 |
| Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe. |
| 8 |
| Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse. |
| 9 |
| “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa, |
| 10 |
| podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje. |
| 11 |
| Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu. |
| 12 |
| Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?” |
| 13 |
| Anafuwula kuti, “Mpachikeni!” |
| 14 |
| Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?” Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!” |
| 15 |
| Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe. |
| 16 |
| Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali. |
| 17 |
| Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake. |
| 18 |
| Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!” |
| 19 |
| Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye. |
| 20 |
| Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike. |
| 21 |
| Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda. |
| 22 |
| Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade) |
| 23 |
| Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe. |
| 24 |
| Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge. |
| 25 |
| Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu. |
| 26 |
| Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: MFUMU YA AYUDA. |
| 27 |
| Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake. |
| 28 |
| (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).” |
| 29 |
| Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu, |
| 30 |
| tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!” |
| 31 |
| Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha! |
| 32 |
| Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira. |
| 33 |
| Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana. |
| 34 |
| Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?” |
| 35 |
| Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.” |
| 36 |
| Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.” |
| 37 |
| Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza. |
| 38 |
| Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. |
| 39 |
| Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.” |
| 40 |
| Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome. |
| 41 |
| Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo. |
| 42 |
| Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira, |
| 43 |
| Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu. |
| 44 |
| Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale. |
| 45 |
| Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe. |
| 46 |
| Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo. |
| 47 |
| Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/mark/015.mp3
16
15