Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo polowanso Iye m'Kapernao atapita masiku ena, kunamveka kuti ali m'nyumba. |
| 2 |
| Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau. |
| 3 |
| Ndipo anadza kwa Iye otenga munthu wodwala manjenje, wonyamulidwa ndi anthu anai. |
| 4 |
| Ndipo pamene sanakhoza kufika kuli Iye, cifukwa ca khamu la anthu, anasasula chindwi pokhala Iye; ndipo pamene anatha kuliboola, anatsitsa mphasa m'mene alinkugonamo wodwala manjenjeyo, |
| 5 |
| Ndipo Yesu pakuona cikhulupiriro cao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, macimo ako akhululukidwa. |
| 6 |
| Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao, |
| 7 |
| Munthu amene atero bwanji? acita mwano; akhoza ndani kukhululukira macimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu? |
| 8 |
| Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwace kuti alikuganizira comweco mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu? |
| 9 |
| Capafupi nciti, kapena kuuza wodwala manjenje kuti, Macimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? |
| 10 |
| Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira macimo pa dziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje), |
| 11 |
| Ndikuuza iwe, Nyamuka, senza mphasa yako, numuke kwanu. |
| 12 |
| Ndipo ananyamuka iye pomwepo, nasenza mphasa, naturuka pamaso pa iwo onse; kotero kuti anadabwa onse, nalemekeza Mulungu, nanena kuti, Zotere sitinaziona ndi kale lonse. |
| 13 |
| Ndipo anaturukanso kunka m'mbali mwa nyanja; ndipo linadza kwa Iye khamu lonse la anthu, ndipo anawaphunzitsa. |
| 14 |
| Ndipo pakumuka, anaona Levi mwana wa Alifeyu alikukhala polandira msonkho, ndipo ananena naye, Tsata Ine. |
| 15 |
| Ndipo ananyamuka namtsata Iye. Ndipo kunali kuti anakhala pakudya m'nyumba mwace, ndipo amisonkho ndi ocimwa ambiri anakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ace, pakuti anali ambiri, ndipo anamtsata Iye. |
| 16 |
| Ndipo alembi a kwa Afarisi, pakuona kuti alinkudya nao ocimwa ndi amisonkho, ananena ndi ophunzira ace, Uyu akudya ndi kumwa nao amisonkho ndi ocimwa. |
| 17 |
| Ndipo pamene Yesu anamva ici, ananena nao, Akulimba safuna sing'anga, koma odwala ndiwo; sindinadza kudzaitana olungama, koma ocimwa. |
| 18 |
| Ndipo ophunzira a Yohane ndi Afarisi analinkusala kudya; ndipo anadza, nanena ndi Iye, Bwanji asala kudya ophunzira a Yohane, ndi ophunzira a Afarisi, koma ophunzira anu sasala kudya? |
| 19 |
| Ndipo Yesu ananena nao, Kodi akhoza kusala kudya anyamata a ukwati pamene mkwati ali pamodzi nao? pokhala ali naye mkwati pamodzi ndi iwo sakhoza kusala. |
| 20 |
| Koma adzadza masiku, pamene mkwati adzacotsedwa kwa iwo, ndipo pamenepo adzasala kudya tsiku lomwelo. |
| 21 |
| Palibe munthu asokerera cigamba ca nsaru yaiwisi pa copfunda cakale; pena cimene coti cidzakonza cizomolapo, catsopanoco cizomoka pa cakaleco, ndipo ciboo cikulapo. |
| 22 |
| Ndipo palibe munthu amatsanulira vinyo watsopano m'matumba akale: pena vinyo adzaphulitsa matumba, ndipo aonongeka vinyo, ndi matumba omwe: koma vinyo watsopano amatsanulira m'matumba atsopano. |
| 23 |
| Ndipo kunali kuti anapita Iye pakati pa minda dzuwa la Sabata; ndipo ophunzira ace poyenda anayamba kubudula ngala za dzinthu. |
| 24 |
| Ndipo Afarisi ananena ndi Iye, Taona, acitiranji cosaloleka kucitika dzuwa la Sabata? |
| 25 |
| Ndipo ananena nao, Simunawerenga konse cimene anacicita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye? |
| 26 |
| Kuti, analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye? |
| 27 |
| Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa cifukwa ca munthu, si munthu cifukwa ca Sabata; |
| 28 |
| motero Mwana wa munthu ali mwini dzuwa la Sabata lomwe. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/mark/002.mp3
16
2