Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo analowanso m'sunagoge; ndipo munali munthu m'menemo ali ndi dzanja lake lopuwala. |
| 2 |
| Ndipo anamuyang'anira Iye, ngati adzamchiritsa tsiku la Sabata; kuti ammange mlandu. |
| 3 |
| Ndipo ananena ndi munthu ali ndi dzanja lopuwala, Taimirira pakati. |
| 4 |
| Ndipo ananena kwa iwo, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchita zabwino, kapena zoipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha? Koma anakhala chete. |
| 5 |
| Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake. |
| 6 |
| Ndipo Afarisi anatuluka, ndipo pomwepo anamkhalira upo ndi Aherode, wakumuononga Iye. |
| 7 |
| Ndipo Yesu anachokako pamodzi ndi ophunzira ake nanka kunyanja: ndipo linamtsata khamu lalikulu la a ku Galileya, ndi a ku Yudeya, |
| 8 |
| ndi a ku Yerusalemu, ndi a ku Idumeya, ndi a ku tsidya lina la Yordani, ndi a kufupi ku Tiro ndi Sidoni, khamu lalikulu, pakumva zazikuluzo anazichita, linadza kwa Iye. |
| 9 |
| Ndipo anati kwa ophunzira ake, kuti kangalawa kamlinde Iye, chifukwa cha khamulo, kuti angamkanikize Iye, |
| 10 |
| pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze. |
| 11 |
| Ndipo mizimu yonyansa, m'mene inamuona Iye, inamgwadira, nifuula, niti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. |
| 12 |
| Ndipo anailimbitsira mau kuti isamuulule Iye. |
| 13 |
| Ndipo anakwera m'phiri, nadziitanira iwo amene anawafuna Iye mwini; ndipo anadza kwa Iye. |
| 14 |
| Ndipo anaika khumi ndi awiri, kuti akhale ndi Iye, ndi kuti akawatume kulalikira, |
| 15 |
| ndi kuti akhale nao ulamuliro wakutulutsa ziwanda. |
| 16 |
| Ndipo Simoni anamutcha Petro; |
| 17 |
| ndi Yakobo mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo, iwo anawatcha Boaneje, ndiko kuti, Ana a bingu; |
| 18 |
| ndi Andrea, ndi Filipo, ndi Bartolomeo, ndi Mateyu, ndi Tomasi, ndi Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo, ndi Simoni Mkanani, |
| 19 |
| ndi Yudasi Iskariote, ndiye amene anampereka Iye. |
| 20 |
| Ndipo anthu ambiri anasonkhananso, kotero kuti sanathe iwo konse kudya. |
| 21 |
| Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka. |
| 22 |
| Ndipo alembi amene adatsika ku Yerusalemu ananena kuti, Ali naye Belezebulu, ndipo, Ndi mkulu wao wa ziwanda atulutsa ziwanda. |
| 23 |
| Ndipo m'mene adawaitana iwo, ananena nao m'mafanizo, Satana angathe bwanji kutulutsa Satana? |
| 24 |
| Ndipo ufumu ukagawanika pa uwu wokha, sukhoza kukhazikika. |
| 25 |
| Ndipo nyumba ikagawanika pa iyo yokha, sikhoza kukhazikika nyumbayo, |
| 26 |
| Ndipo Satana akadziukira mwini yekha, nagawanika, sakhoza kukhazikika, koma atsirizika. |
| 27 |
| Komatu palibe munthu akhoza kulowa m'nyumba ya mwini mphamvu, ndi kufunkha akatundu ake, koma athange wamanga mwini mphamvuyo; ndipo pamenepo adzafunkha za m'nyumba mwake. |
| 28 |
| Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo; |
| 29 |
| koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha; |
| 30 |
| pakuti adanena, Ali ndi mzimu wonyansa. |
| 31 |
| Ndipo anadza amake ndi abale ake; naima kunja, namtumira uthenga kumuitana. |
| 32 |
| Ndipo anthu ambiri anakhala pansi pomzinga; nanena kwa Iye, Onani, amanu ndi abale anu ali kunja akufunani Inu. |
| 33 |
| Ndipo anawayankha nanena, Amai wanga ndi abale anga ndani? |
| 34 |
| Ndipo anawaunguzaunguza iwo akumzingawo, nanena, Taonani, amai wanga ndi abale anga. |
| 35 |
| Pakuti aliyense achita chifuniro cha Mulungu, yemweyo ndiye mbale wanga, ndi mlongo, ndi amai. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/mark/003.mp3
16
3