Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. |
| 2 |
| Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. |
| 3 |
| Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.” |
| 4 |
| Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete. |
| 5 |
| Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira. |
| 6 |
| Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu. |
| 7 |
| Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. |
| 8 |
| Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. |
| 9 |
| Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. |
| 10 |
| Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. |
| 11 |
| Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” |
| 12 |
| Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani. |
| 13 |
| Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. |
| 14 |
| Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira |
| 15 |
| ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. |
| 16 |
| Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); |
| 17 |
| Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); |
| 18 |
| Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, |
| 19 |
| ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye. |
| 20 |
| Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. |
| 21 |
| Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.” |
| 22 |
| Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.” |
| 23 |
| Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? |
| 24 |
| Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. |
| 25 |
| Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. |
| 26 |
| Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. |
| 27 |
| Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. |
| 28 |
| Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, |
| 29 |
| koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.” |
| 30 |
| Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.” |
| 31 |
| Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. |
| 32 |
| Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.” |
| 33 |
| Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?” |
| 34 |
| Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga! |
| 35 |
| Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.” |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/mark/003.mp3
16
3