Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa. |
| 2 |
| Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa, |
| 3 |
| amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo; |
| 4 |
| pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. |
| 5 |
| Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala. |
| 6 |
| Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye; |
| 7 |
| ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze. |
| 8 |
| Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu. |
| 9 |
| Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri. |
| 10 |
| Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko. |
| 11 |
| Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri. |
| 12 |
| Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo. |
| 13 |
| Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m'nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m'nyanja. |
| 14 |
| Ndipo akuziweta anathawa, nauza m'mudzi, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho. |
| 15 |
| Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo. |
| 16 |
| Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo. |
| 17 |
| Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m'malire ao. |
| 18 |
| Ndipo m'mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye. |
| 19 |
| Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo. |
| 20 |
| Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa. |
| 21 |
| Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja. |
| 22 |
| Ndipo anadzako mmodzi wa akulu a sunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri, |
| 23 |
| nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo. |
| 24 |
| Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye. |
| 25 |
| Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, |
| 26 |
| ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing'anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang'ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula, |
| 27 |
| m'mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m'khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake. |
| 28 |
| Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa. |
| 29 |
| Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m'thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake. |
| 30 |
| Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m'khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga? |
| 31 |
| Ndipo ophunzira ake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani? |
| 32 |
| Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi. |
| 33 |
| Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse. |
| 34 |
| Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako. |
| 35 |
| M'mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi? |
| 36 |
| Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha. |
| 37 |
| Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo. |
| 38 |
| Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri. |
| 39 |
| Ndipo m'mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m'tulo. |
| 40 |
| Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m'mene munali mwanayo. |
| 41 |
| Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye, Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka. |
| 42 |
| Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu. |
| 43 |
| Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/mark/005.mp3
16
5