Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipo ophunzira ake anamtsata. |
| 2 |
| Ndipo pofika tsiku la Sabata, anayamba kuphunzitsa m'sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake? |
| 3 |
| Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye. |
| 4 |
| Ndipo Yesu ananena kwa iwo, Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m'dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m'nyumba yake. |
| 5 |
| Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa. |
| 6 |
| Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m'midzi yozungulirapo, naphunzitsa. |
| 7 |
| Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa; |
| 8 |
| ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m'lamba lao; |
| 9 |
| koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri. |
| 10 |
| Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m'nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako. |
| 11 |
| Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo. |
| 12 |
| Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima. |
| 13 |
| Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa. |
| 14 |
| Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye. |
| 15 |
| Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo. |
| 16 |
| Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo. |
| 17 |
| Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m'nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye. |
| 18 |
| Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu. |
| 19 |
| Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze; |
| 20 |
| pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye. |
| 21 |
| Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya; |
| 22 |
| ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe. |
| 23 |
| Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga. |
| 24 |
| Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi. |
| 25 |
| Ndipo pomwepo analowa m'mangum'mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale. |
| 26 |
| Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza. |
| 27 |
| Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m'nyumba yandende; |
| 28 |
| natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake. |
| 29 |
| Ndipo m'mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m'manda. |
| 30 |
| Ndipo atumwi anasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa. |
| 31 |
| Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya. |
| 32 |
| Ndipo anachokera m'ngalawa kunka kumalo achipululu padera. |
| 33 |
| Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m'midzi monse, nawapitirira. |
| 34 |
| Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri. |
| 35 |
| Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu; |
| 36 |
| muwauze kuti amuke, alowe kumilaga ndi kumidzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya. |
| 37 |
| Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya? |
| 38 |
| Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani, mukaone. Ndipo m'mene anadziwa ananena, Isanu, ndi nsomba ziwiri. |
| 39 |
| Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu. |
| 40 |
| Ndipo anakhala pansi mabungwemabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu. |
| 41 |
| Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang'ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo. |
| 42 |
| Ndipo anadya iwo onse, nakhuta. |
| 43 |
| Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba. |
| 44 |
| Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu. |
| 45 |
| Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m'ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m'mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke. |
| 46 |
| Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera. |
| 47 |
| Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda. |
| 48 |
| Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire; |
| 49 |
| koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula: |
| 50 |
| pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope. |
| 51 |
| Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m'ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukulu mwa iwo okha; |
| 52 |
| pakuti sanazindikire za mikateyo, koma mitima yao inauma. |
| 53 |
| Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padooko. |
| 54 |
| Ndipo pamene anatuluka m'ngalawa anamzindikira pomwepo, |
| 55 |
| nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye. |
| 56 |
| Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena m'milaga, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/mark/006.mp3
16
6