Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu, |
| 2 |
| ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba. |
| 3 |
| Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu; |
| 4 |
| ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa. |
| 5 |
| Ndipo Afarisi ndi alembi anamfunsa Iye, kuti, Bwanji ophunzira anu satsata mwambo wa akulu, koma akudya mkate wao ndi m'manja mwakuda? |
| 6 |
| Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. |
| 7 |
| Koma andilambira Iye kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu. |
| 8 |
| Musiya lamulo la Mulungu, nimusunga mwambo wa anthu. |
| 9 |
| Ndipo ananena nao, Bwino mukaniza lamulo la Mulungu, kuti musunge mwambo wanu. |
| 10 |
| Pakuti Mose anati, Lemekeza atate wako ndi amai ako; ndipo iye wakunenera zoipa atate wake kapena amai wake, afe ndithu; |
| 11 |
| koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine, |
| 12 |
| simulolanso kumchitira kanthu atate wake kapena amai wake; |
| 13 |
| muyesa achabe mau a Mulungu mwa mwambo wanu, umene munaupereka: ndi zinthu zotere zambiri muzichita. |
| 14 |
| Ndipo anadziitaniranso khamu la anthu, nanena nao, Mverani Ine nonsenu, ndipo dziwitsani: |
| 15 |
| kulibe kanthu kunja kwa munthu kukalowa mwa iye, kangathe kumdetsa: koma zinthu zakutuluka mwa munthu, ndizo zakumdetsa munthu. |
| 16 |
| 17 |
| Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo. |
| 18 |
| Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye; |
| 19 |
| chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse. |
| 20 |
| Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu. |
| 21 |
| Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere, |
| 22 |
| zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa: |
| 23 |
| zoipa izi zonse zituluka m'kati, nizidetsa munthu. |
| 24 |
| Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika. |
| 25 |
| Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake. |
| 26 |
| Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake. |
| 27 |
| Ndipo ananena naye, Baleka, athange akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu. |
| 28 |
| Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Ine Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana. |
| 29 |
| Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi. |
| 30 |
| Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka. |
| 31 |
| Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli. |
| 32 |
| Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye. |
| 33 |
| Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake: |
| 34 |
| nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka. |
| 35 |
| Ndipo makutu ake anatsegula, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire. |
| 36 |
| Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana. |
| 37 |
| Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/mark/007.mp3
16
7