Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo khamu lonselo Iinanyamuka kupita naye kwa Pilato. |
| 2 |
| Ndipo anayamba kumnenera iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu. |
| 3 |
| Ndipo Pilato anamfunsa iye, nanena, Kodindiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo iye anamyankha nati, Mwatero. |
| 4 |
| Ndipo Pilato anati kwa ansembe akuru ndi makamu a anthu, Ndiribe kupeza cifukwa ca mlandu ndi munthu uyu. |
| 5 |
| Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa m'Yudeya lonse, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe. |
| 6 |
| Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya. |
| 7 |
| Ndipo m'mene anadziwa kuti ali wa m'ulamuliro wace wa Herode, anamtumiza iye kwa Herode, amene anali iye mwini ku Yerusalemu masiku awa, |
| 8 |
| Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya iye, cifukwa anamva za iye; nayembekeza kuona cizindikilo cina cocitidwa ndi iye. |
| 9 |
| Ndipo anamfunsa iye mau ambiri; koma iye sanamyankha kanthu. |
| 10 |
| Ndipo ansembe akuru ndi alembi anaimirira, namnenera iye kolimba. |
| 11 |
| Ndipo Herode ndi asilikari ace anampeputsa iye, namnyoza, nambveka iye copfunda conyezimira, nambwezera kwa Pilato. |
| 12 |
| Ndipo Herode ndi Pilato anaci-I tana cibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana. |
| 13 |
| Ndipo Pilato anaitana ansembe akuru, ndi akuru, ndi anthu, asonkhane, |
| 14 |
| nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu cifukwa ca zinthu zimene mumnenera; |
| 15 |
| inde, nga khale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera iye kwa ife; ndipo taonani, sanacita iye kanthu kakuyenera kufa. |
| 16 |
| Cifukwacace ndidzamkwapula ndi kununasula iye. [ |
| 17 |
| ] |
| 18 |
| Koma iwo onse pamodzi anapfuula, nati, Cotsani munthu uyu, mutimasulire Baraba; |
| 19 |
| ndiye munthu anaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko m'mudzi ndi ca kupha munthu. |
| 20 |
| Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu; |
| 21 |
| koma iwo anapfuula, nanena, Mpacikeni, mpacikeni pamtanda. |
| 22 |
| Ndipo anati kwa iwo nthawi yacitatu, Nanga munthuyu anacita coipa ciani? Sindinapeza cifukwa ca kufera iye; cotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula. |
| 23 |
| Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti iye apacikidwe, Ndipo mau ao analakika. |
| 24 |
| Ndipo Pilato anaweruza kuti cimene alikufunsa cicitidwe. |
| 25 |
| Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m'ndende cifukwa ca mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa cifuniro cao. |
| 26 |
| Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kurene, alikucokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pace pa Yesu, |
| 27 |
| Ndipo unamtsata unyinji waukuru wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pacifuwa, namlirira iye. |
| 28 |
| Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana akazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu. |
| 29 |
| Cifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa. |
| 30 |
| Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife. |
| 31 |
| Pakuti ngati azicitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma? |
| 32 |
| Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ocita zoipa; anatengedwa pamodzi ndi iye kuti aphedwe. |
| 33 |
| Ndipo pamene anafika ku malo dzina lace Bade, anampacika iye pamtanda pomwepo, ndi ocita zoipa omwe, mmodzi ku dzanja lamanja ndi wina kulamanzere. |
| 34 |
| Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa cimene acita. Ndipo anagawana zobvala zace, poyesa maere. |
| 35 |
| Ndipo anthu anaima alikupenya, Ndi akurunso anamlalatira iye nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Kristu wa Mulungu, wosankhidwa wace. |
| 36 |
| Ndipo asilikarinso anamnyoza, nadza kwa iye, nampatsa vinyo wosasa, |
| 37 |
| nanena, Ngati Iwe ndiwe Mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha. |
| 38 |
| Ndipo kunalinso lembo pamwamba pace, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YAAYUDA. |
| 39 |
| Ndipo mmodzi wa ocita zoipa anapacikidwawo anamcitira iye mwano nanena, Kodi suli Kristu Iwe? udzipulumutse wekha ndi ife. |
| 40 |
| Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m'kulangika komweku? |
| 41 |
| Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tirikulandira zoyenera zimene tinazicita: koma munthu uyu sanacita kanthu kolakwa. |
| 42 |
| Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukileni m'mene mulowa Ufumuwanu. |
| 43 |
| Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine m'Paradaiso. |
| 44 |
| Ndipo ora lace pamenepo linali ngati lacisanu ndi cimodzi. Ndipo panali mdima pa dziko lonse kufikira ora lacisanu ndi cinai, ndipo dzuwa linada. |
| 45 |
| Ndipo nsaru yocinga ya m'Kacisi inang'ambika pakati. |
| 46 |
| Ndipo pamene Yesu anapfuula ndi mau akuru, anati, 1 Atate, m'manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wace. |
| 47 |
| Ndipo 2 pamene kenturiyo anaona cinacitikaco, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama. |
| 48 |
| Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ici, pamene anaona zinacitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pacifuwa. |
| 49 |
| Ndipo 3 omdziwa iye onse, ndi akazi amene adamtsata kucokera ku Galileya, anaima kutari, naona zinthu izi. |
| 50 |
| Ndipo taonani, munthu dzina lace Yosefe, ndiye mkuru wa mirandu, munthu wabwino ndi wolungama |
| 51 |
| (amene sanabvomereza kuweruza kwao ndi nchito yao) wa ku Arimateya, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu, |
| 52 |
| yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wace wa Yesu. |
| 53 |
| Ndipo 4 anautsitsa, naukulunga m'nsaru yabafuta, nauika m'manda osemedwa m'mwala, m'menemo sanaika munthu ndi kale lonse. |
| 54 |
| Ndipo panali tsiku lokonzera, ndi Sabata linayandikira. |
| 55 |
| Ndipo 5 akazi, amene anacokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wace. |
| 56 |
| Ndipo anapita kwao, 6 nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula 7 monga mwa lamulo. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/luke/023.mp3
24
23