Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani Inenso. |
| 2 |
| M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukukonzerani inu malo. |
| 3 |
| Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, ndidzabweranso, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso. |
| 4 |
| Ndipo kumene ndinkako Ine, mudziwa njira yace. |
| 5 |
| Tomasi ananena ndi Iye, Ambuye, sitidziwa kumene munkako; tidziwa njira bwanji? |
| 6 |
| Yesu ananena naye, ine ndinenjira, ndi coonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine. |
| 7 |
| Mukadazindikira ine mukadadziwa Atate wanganso; kuyambira tsopano mumzindikira iye, ndipo mwamuona iye. |
| 8 |
| Filipo ananena ndi iye, Ambuye, tionetsereni ife Atate, ndipo citikwanira. |
| 9 |
| Yesu ananena naye, Kodi ndiri ndiinu nthawi yaikuru yotere, ndipo sunandizindikira, Filipo? iye amene wandiona Ine waona Atate; unena iwe bwanji, Mutionetsere Atate? |
| 10 |
| Sukhulupirira kodi kuti ndiri Ine mwa Atate, ndi Atate ali mwa Ine? Mau amene ndinena Ine kwa inu sindilankhula kwa Ine ndekha; koma Atate wokhala mwa Ine acita nchito zace. |
| 11 |
| Khulupirirani Ine, kuti Inendiri mwa Atate ndi Atate ali mwa Ine; koma ngati si comweco, khulupirirani Ine cifukwa ca nchito zomwe. |
| 12 |
| Indetu, indetu, ndinena kwa inu, Wokhulupirira Ine, nchito zimene ndicita Ine adzazicitanso iyeyu; ndipo adzacita zoposa izi; cifukwa ndipita Ine kwa Atate. |
| 13 |
| Ndipo cimene ciri conse mukafunse m'dzina langa, ndidzacicita, kuti Atate akalemekezedwe mwa Mwana. |
| 14 |
| Ngati mudzapempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita. |
| 15 |
| Ngati mukonda Ine, sungani malamulo anga. |
| 16 |
| Ndipo Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu Nkhoswe yina, kuti akhale ndi inu ku nthawi yonse, |
| 17 |
| ndiye Mzimu wa coonadi; amene dziko lapansi silingathe kumlandira, pakuti silimuona iye, kapena kumzindikira iye. Inu mumzindikira iye; cifukwa akhala ndi inu nadzakhala mwa inu. |
| 18 |
| Sindidza-kusiyani inu mukhale ana amasiye; ndidza kwa inu. |
| 19 |
| Katsala kanthawi, ndipo dziko lapansi silindionanso Ine; koma inu mundiona; popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo. |
| 20 |
| Tsiku lo mwelo mudzazindikira kuti ndiri Ine mwa Atate wanga, ndi inu mwa Ine, ndi Ine mwa inu. |
| 21 |
| Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine; koma wondikonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo line ndidzamkonda, ndipo ndidzadzionetsandekha kwa iye. |
| 22 |
| Yudase, si Isikariote, ananena ndi iye, Ambuye, cacitika ciani kuti muziti mudzionetsa nokha kwa ife, koma si kwa dziko lapansi? |
| 23 |
| Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo. |
| 24 |
| Wosandikonda Ine sasunga mau anga; ndipo 1 mau amene mumva sali mau anga, koma a Atate wondituma Ine. |
| 25 |
| Izi ndalankhula nanu, pakukhala ndi inu. |
| 26 |
| Koma 2 Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamtuma m'dzina langa, 3 Iyeyo adzaphunzitsa Inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu. |
| 27 |
| 4 Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; Ine sindikupatsani inu monga dziko lapansi lipatsa. 5 Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha. |
| 28 |
| Mwamva kuti Ine ndinanena kwa inu, 6 Ndimuka, ndipo ndidza kwa inu. Mukadandikonda Ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; 7 pakuti Atate ali wamkuru ndi Ine. |
| 29 |
| Ndipo tsopano 8 ndakuuzani cisanacitike, kuti pamene citacitika mukakhulupire. |
| 30 |
| Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti 9 mkuru wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine; |
| 31 |
| koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti ndikonda Atate, ndikuti 10 ndicita monga momwe Atate wandilamulira. Nyamukani, tizimuka kucokera kuno. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/john/014.mp3
21
14