|
| 1 |
|
| Pamene Yesu ankayenda, adaona munthu wa khungu lobadwa nalo. |
|
| 2 |
|
| Ophunzira ake adamufunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi adachimwa ndani kuti munthu ameneyu abadwe wakhungu? Adachimwa ndi iyeyu kapena makolo ake?” |
|
| 3 |
|
| Yesu adati, “Sikuti iyeyu adachimwa kapena makolo ake ai. Koma adabadwa wakhungu kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iye. |
|
| 4 |
|
| Kukali usana tizigwira ntchito za Atate amene adandituma. Usiku ukudza pamene munthu sangathe kugwira ntchito. |
|
| 5 |
|
| Pamene ndili pansi pano, ndine kuŵala kounikira anthu onse.” |
|
| 6 |
|
| Atanena zimenezi, Yesu adalavulira malovu pansi, nakanda thope ndi malovuwo. Kenaka adapaka thopelo m'maso mwa munthuyo, |
|
| 7 |
|
| namuuza kuti, “Pita ukasambe ku dziŵe la Siloamu.” (Tanthauzo la Siloamu ndiye kuti, Wotumidwa.) Munthuyo adapitadi, adakasamba, nabwerako akupenya. |
|
| 8 |
|
| Pamenepo anzake ndi anthu amene kale ankamuwona akupemphapempha adati, “Kodi uyu si uja ankakhala pansi apa nkumangopempha?” |
|
| 9 |
|
| Ena adati, “Ndiye amene.” Ena nkumati, “Iyai, akungofanafana naye.” Koma mwiniwakeyo adati, “Ai ndithu, ndine amene.” |
|
| 10 |
|
| Apo anthu aja adamufunsa kuti, “Nanga maso ako apenya bwanji?” |
|
| 11 |
|
| Iyeyo adati, “Munthu uja amati Yesuyu anakanda thope nalipaka m'maso mwangamu. Kenaka anandiwuza kuti, ‘Pita, ukasambe ku Siloamu. Ndinapitadi, ndipo nditasamba, ndayamba kupenya.’ ” |
|
| 12 |
|
| Anthuwo adamufunsa kuti, “Iyeyo ali kuti?” Munthu uja adati, “Kaya, sindikudziŵa.” |
|
| 13 |
|
| Tsono munthu uja kale sankapenyayu adapita naye kwa Afarisi. |
|
| 14 |
|
| Tsiku limene Yesu adaakanda thope namchiritsalo linali la Sabata. |
|
| 15 |
|
| Tsono Afarisi nawonso adamufunsa munthu uja kuti, “Iwe, wapenya bwanji?” Iye adaŵauza kuti, “Anandipaka thope m'maso mwanga, ine nkukasamba, ndipo tsopano ndikupenya.” |
|
| 16 |
|
| Afarisi ena adati, “Munthu amene uja ngwosachokera kwa Mulungu, chifukwa satsata lamulo lokhudza tsiku la Sabata.” Koma ena adati, “Kodi inu, munthu wochimwa nkuchita zizindikiro zozizwitsa zotere?” Choncho panali kutsutsana. |
|
| 17 |
|
| Tsono Afarisi aja adamufunsanso munthu uja kale sankapenyayu, adati, “Kodi iweyo ukuti chiyani za Iyeyo, m'mene wakuchiritsamu?” Iye adati, “Ndi mneneritu basi.” |
|
| 18 |
|
| Koma akulu a Ayudawo sadakhulupirire kuti munthuyo kale sankapenya ndipo tsopano akupenya, mpaka adaitanitsa makolo ake. |
|
| 19 |
|
| Tsono adaŵafunsa kuti, “Kodi inu, uyu ndi mwana wanu? Ndiye mukuti adaabadwadi wosapenya? Nanga zatani kuti tsopano akupenya?” |
|
| 20 |
|
| Makolo ake adati, “Chimene tikudziŵa ife nchakuti ameneyu ndi mwana wathu, ndipo adaabadwadi wosapenya. |
|
| 21 |
|
| Koma kuti tsopano akupenya, sitikudziŵa m'mene zachitikira. Zoti wamupenyetsa ndani kaya, ife sitikudziŵanso. Mufunseni mwiniwakeyu, ngwamkulu, afotokoze yekha.” |
|
| 22 |
|
| Makolo akewo adaatero chifukwa ankaopa akulu a Ayuda. Pakuti Ayuda anali atapangana kale kuti, ngati munthu adzavomereza kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja, adzamdula ku mpingo. |
|
| 23 |
|
| Nchifukwa chake makolo akewo adati, “Ngwamkulu, mufunseni mwiniwakeyu.” |
|
| 24 |
|
| Pamenepo Ayuda aja adamuitana kachiŵiri munthu uja kale sankapenyayu, namuuza kuti, “Lemekeza Mulungu, ndipo unene zoona. Ife tikudziŵa kuti munthu amene uja ngwochimwa.” |
|
| 25 |
|
| Iye adati, “Zakuti Iye ngwochimwa, ine sindikudziŵa. Chinthu chimodzi chokha ndikudziŵa, kuti kale ndinali wosapenya, koma tsopano ndikupenya.” |
|
| 26 |
|
| Iwo adamufunsa kuti, “Kodi anachita chiyani pamene anakupenyetsa?” |
|
| 27 |
|
| Iye adati, “Ndakuuzani kale, koma simumasamalako. Nanga chifukwa chiyani mukufuna kuzimvanso? Kapenatu nanunso mukufuna kukhala ophunzira ake eti?” |
|
| 28 |
|
| Pamenepo iwo adayamba kumlalatira, adati, “Wophunzira wake ndi iweyo. Ife ndifetu ophunzira a Mose. |
|
| 29 |
|
| Tikudziŵa kuti Mulungu adalankhula ndi Mose, koma uyu sitikudziŵa kumene wachokera.” |
|
| 30 |
|
| Munthuyo adati, “Pakudabwitsatu mpamenepa: kuti inuyo simukudziŵa kumene Iye wachokera, komabe wandipenyetsa. |
|
| 31 |
|
| Timadziŵa kuti Mulungu samvera anthu ochimwa. Koma munthu akasamala za Mulungu, nachita zimene Mulungu afuna, Mulungu amamumvera. |
|
| 32 |
|
| Nkale lomwe sikudamveke konse kuti wina adapenyetsa munthu wakhungu. |
|
| 33 |
|
| Munthu ameneyu akadapanda kuchokera kwa Mulungu, sakadatha konse kuchita kanthu.” |
|
| 34 |
|
| Iwo adati, “Iwe udabadwa m'machimo okhaokha. Ndiye iweyo nkutiphunzitsa ife?” Atatero adamtulutsa nkumudula ku mpingo. |
|
| 35 |
|
| Yesu adamva kuti Ayuda amtulutsa ndi kumdula ku mpingo munthu uja. Tsono pamene adampeza, adamufunsa kuti, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?” |
|
| 36 |
|
| Iye adati, “Ambuye, mundiwuzetu ndani Iyeyo, kuti ndimkhulupirire.” |
|
| 37 |
|
| Yesu adamuuza kuti, “Wamuwona kale, ndi yemwe akulankhula nawe.” |
|
| 38 |
|
| Iye adati, “Ambuye, ndikukhulupirira.” Atatero adamgwadira. |
|
| 39 |
|
| Tsono Yesu adati, “Ndidabwera pansi pano kudzaweruza, kuti osapenya apenye, ndipo openya achite khungu.” |
|
| 40 |
|
| Afarisi ena amene anali pafupi naye, atamva zimenezi adamufunsa kuti, “Kodi monga ifenso ndife akhungu?” |
|
| 41 |
|
| Yesu adati, “Mukadakhala akhungu, bwenzi mulibe mlandu. Koma chifukwa mukuti, ‘Tikupenya,’ ndiye kuti mlandu wanu ulipobe.” |
|
|
|
|