|
| 1 |
|
| Ndipo potero Myuda aposa ninji? Kapena mdulidwe upindulanji? |
|
| 2 |
|
| Zambiri monsemonse: choyamba, kuti mau a Mulungu anaperekedwa kwa iwo. |
|
| 3 |
|
| Nanga bwanji ngati ena sanakhulupirira? Kodi kusakhulupirira kwao kuyesa chabe chikhulupiriko cha Mulungu? |
|
| 4 |
|
| Msatero ai. Koma Mulungu akhale woona, ndimo anthu onse akhale onama; monga kwalembedwa, Kuti Inu mukayesedwe wolungama m'maneno anu, ndi kuti mukalakike m'mene muweruzidwa. |
|
| 5 |
|
| Koma ngati chosalungama chathu chitsimikiza chilungamo cha Mulungu, tidzatani ife? Kodi ali wosalungama Mulungu, amene afikitsa mkwiyo? (Ndilankhula umo anenera munthu). |
|
| 6 |
|
| Msatero ai. Ngati kotero, Mulungu adzaweruza bwanji mlandu wa dziko lapansi? |
|
| 7 |
|
| Pakuti ngati choonadi cha Mulungu chichulukitsa ulemerero wake chifukwa cha bodza langa, nanga inenso ndiweruzidwa bwanji monga wochimwa? |
|
| 8 |
|
| Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama. |
|
| 9 |
|
| Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo; |
|
| 10 |
|
| monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi; |
|
| 11 |
|
| palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu; |
|
| 12 |
|
| onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu. |
|
| 13 |
|
| M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao; |
|
| 14 |
|
| m'kamwa mwao mudzala ndi zotemberera ndi zowawa; |
|
| 15 |
|
| miyendo yao ichita liwiro kukhetsa mwazi; |
|
| 16 |
|
| kusakaza ndi kusauka kuli m'njira zao; |
|
| 17 |
|
| ndipo njira ya mtendere sanaidziwa; |
|
| 18 |
|
| kumuopa Mulungu kulibe pamaso pao. |
|
| 19 |
|
| Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu; |
|
| 20 |
|
| chifukwa kuti pamaso pake palibe munthu adzayesedwa wolungama ndi ntchito za lamulo; pakuti uchimo udziwika ndi lamulo. |
|
| 21 |
|
| Koma tsopano chilungamo cha Mulungu chaoneka chopanda lamulo, chilamulo ndi aneneri achitira ichi umboni; |
|
| 22 |
|
| ndicho chilungamo cha Mulungu chimene chichokera mwa chikhulupiriro cha pa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira; pakuti palibe kusiyana; |
|
| 23 |
|
| pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; |
|
| 24 |
|
| ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; |
|
| 25 |
|
| amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; |
|
| 26 |
|
| kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu. |
|
| 27 |
|
| Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro. |
|
| 28 |
|
| Pakuti timuyesa munthu wolungama chifukwa cha chikhulupiriro, wopanda ntchito za lamulo. |
|
| 29 |
|
| Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso: |
|
| 30 |
|
| ngatitu ndiye Mulungu mmodzi, amene adzawayesa amdulidwe olungama ndi chikhulupiriro, ndi akusadulidwa mwa chikhulupiriro. |
|
| 31 |
|
| Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo. |
|
|
|
|