Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi cisoni. |
| 2 |
| Pakuti ngati ine ndimvetsa inu cisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, kama iye amene ndammvetsa cisoni? |
| 3 |
| Ndipo ndinalemba ici comwe, kuti pakudza ndisakhale naco cisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti cimwemwe canga ndi canu ca inu nonse. |
| 4 |
| Pakuti m'cisautso cambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni cisoni, koma kuti mukadziwe cikondi ca kwa inu, cimene ndiri naco koposa. |
| 5 |
| Koma ngati wina wacititsa cisoni, sanacititsa cisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse. |
| 6 |
| Kwa wotereyo cilango ici cidacitika ndi ambiri cikwanira; |
| 7 |
| kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo mgamizidwe ndi cisoni cocurukaco. |
| 8 |
| Cifukwa cace ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo cikondi canu. |
| 9 |
| Pakuti cifukwa ca ici ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse. |
| 10 |
| Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti cimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndacicita cifukwa ca inu, pamasopa Kristu; |
| 11 |
| kuti asaticenierere Satana; pakuti sitikhala osadziwa macenjerero ace. |
| 12 |
| Koma pamene ndinadza ku Trowa kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Kristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye, |
| 13 |
| ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Makedoniya. |
| 14 |
| Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse. |
| 15 |
| Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa; |
| 16 |
| koma kwa ena pfungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi? |
| 17 |
| Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akucita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa coona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/2corinthians/002.mp3
13
2