Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi chisoni. |
| 2 |
| Pakuti ngati ine ndimvetsa inu chisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, koma iye amene ndammvetsa chisoni? |
| 3 |
| Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse. |
| 4 |
| Pakuti m'chisautso chambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi cha kwa inu, chimene ndili nacho koposa. |
| 5 |
| Koma ngati wina wachititsa chisoni, sanachititsa chisoni ine, koma pena (kuti ndisasenzetse) inu nonse. |
| 6 |
| Kwa wotereyo chilango ichi chidachitika ndi ambiri chikwanira; |
| 7 |
| kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho. |
| 8 |
| Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu. |
| 9 |
| Pakuti chifukwa cha ichi ndalembanso, kuti ndidziwe mayesedwe anu, ngati muli omvera m'zonse. |
| 10 |
| Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti chimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndachichita chifukwa cha inu, pamaso pa Khristu; |
| 11 |
| kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake. |
| 12 |
| Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye, |
| 13 |
| ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya. |
| 14 |
| Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'chigonjetso mwa Khristu, namveketsa fungo la chidziwitso chake mwa ife pamalo ponse. |
| 15 |
| Pakuti ife ndife fungo labwino la Khristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena fungo la imfa kuimfa; |
| 16 |
| koma kwa ena fungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi? |
| 17 |
| Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2corinthians/002.mp3
13
2