Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? |
| 2 |
| Inu ndinu kalata wathu, wolembedwa mu mitima yathu, wodziwika ndi wowerengedwa ndi anthu onse; |
| 3 |
| popeza mwaonetsedwa kuti muli kalata wa Khristu, wakumtumikira ndi ife, wosalembedwa ndi kapezi iai, koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo; wosati m'magome amiyala, koma m'magome a mitima yathupi. |
| 4 |
| Ndipo kulimbika kotere kwa Mulungu tili nako mwa Khristu: |
| 5 |
| si kuti tili okwanira pa ife tokha, kuyesera kanthu monga mochokera mwa ife tokha; kukwanira kwathu kuchokera kwa Mulungu; |
| 6 |
| amenenso anatikwaniritsa ife tikhale atumiki a pangano latsopano; si la chilembo, koma la mzimu; pakuti chilembo chipha, koma mzimu uchititsa moyo. |
| 7 |
| Koma ngati utumiki wa imfa wolembedwa ndi wolochedwa m'miyala, unakhala m'ulemerero, kotero kuti ana a Israele sanathe kuyang'anitsa pa nkhope yake ya Mose, chifukwa cha ulemerero wa nkhope yake, umene unalikuchotsedwa: |
| 8 |
| koposa kotani nanga utumiki wa Mzimu udzakhala m'ulemerero? |
| 9 |
| Pakuti ngati utumiki wa chitsutso unali wa ulemerero, makamaka utumiki wa chilungamo uchulukira muulemerero kwambiri. |
| 10 |
| Pakutinso chimene chinachitidwa cha ulemerero sichinachitidwa cha ulemerero m'menemo, chifukwa cha ulemerero woposawo. |
| 11 |
| Pakuti ngati chimene chilikuchotsedwa chinakhala m'ulemerero, makamaka kwambiri chotsalacho chili m'ulemerero. |
| 12 |
| Pokhala nacho tsono chiyembekezo chotere, tilankhula ndi kukhazikika mtima kwakukulu, |
| 13 |
| ndipo si monga Mose, amene anaika chophimba pa nkhope yake, kuti ana a Israele asayang'anitse pa chimaliziro cha chimene chinalikuchotsedwa; |
| 14 |
| koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu. |
| 15 |
| Koma kufikira lero, pamene awerengedwa Mose, chophimba chigona pamtima pao. |
| 16 |
| Koma pamene akatembenukira kwa Mulungu, chophimbacho chichotsedwa. |
| 17 |
| Koma Ambuye ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye pali ufulu. |
| 18 |
| Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2corinthians/003.mp3
13
3