Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Chifukwa chake popeza tili nao utumiki umene, monga talandira chifundo, sitifooka; |
| 2 |
| koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbu mtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu. |
| 3 |
| Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; |
| 4 |
| mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire. |
| 5 |
| Pakuti tilalikira si za ife tokha, koma Yesu Khristu Ambuye, ndi ife tokha akapolo anu, chifukwa cha Khristu. |
| 6 |
| Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu. |
| 7 |
| Koma tili nacho chuma ichi m'zotengera zadothi, kuti ukulu woposa wamphamvu ukhale wa Mulungu, wosachokera kwa ife; |
| 8 |
| ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; |
| 9 |
| olondoleka, koma osatayika; ogwetsedwa, koma osaonongeka; |
| 10 |
| nthawi zonse tilikusenzasenza m'thupi kufa kwake kwa Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi mwathu. |
| 11 |
| Pakuti ife amene tili ndi moyo tiperekeka kuimfa nthawi zonse, chifukwa cha Yesu, kuti moyonso wa Yesu uoneke m'thupi lathu lakufa. |
| 12 |
| Chotero imfa ichita mwa ife, koma moyo mwa inu. |
| 13 |
| Koma pokhala nao mzimu womwewo wa chikhulupiriro, monga mwa cholembedwacho, ndinakhulupirira, chifukwa chake ndinalankhula; ifenso tikhulupirira, chifukwa chake tilankhula; |
| 14 |
| podziwa kuti Iye amene anaukitsa Ambuye Yesu adzaukitsa ifenso pamodzi ndi Yesu, nadzatiikapo pamodzi ndi inu. |
| 15 |
| Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu. |
| 16 |
| Chifukwa chake sitifooka; koma ungakhale umunthu wathu wakunja uvunda, wa m'kati mwathu ukonzedwa kwatsopano tsiku ndi tsiku. |
| 17 |
| Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero; |
| 18 |
| popeza sitipenyerera zinthu zooneka, koma zinthu zosaoneka; pakuti zinthu zooneka zili za nthawi, koma zinthu zosaoneka zili zosatha. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2corinthians/004.mp3
13
4