Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Ndipo tikudziwitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Masedoniya, |
| 2 |
| kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao. |
| 3 |
| Pakuti monga mwa mphamvu yao, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yao, |
| 4 |
| anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima; |
| 5 |
| ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu. |
| 6 |
| Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso. |
| 7 |
| Koma monga muchulukira m'zonse, m'chikhulupiriro, ndi m'mau, ndi m'chidziwitso, ndi m'khama lonse, ndi m'chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso m'chisomo ichi. |
| 8 |
| Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa mwa khama la ena choonadi cha chikondi chanunso. |
| 9 |
| Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera. |
| 10 |
| Ndipo m'menemo nditchula choyesa ine; pakuti chimene chipindulira inu, amene munayamba kale chaka chapitachi si kuchita kokha, komanso kufunira. |
| 11 |
| Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m'chimene muli nacho. |
| 12 |
| Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa. |
| 13 |
| Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe; |
| 14 |
| koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusowa kwao nthawi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwao kukwanire kusowa kwanu. |
| 15 |
| Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, Wosonkhetsa chambiri sichinamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang'ono sichinamsowa. |
| 16 |
| Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito. |
| 17 |
| Pakutitu analandira kudandaulira kwathu; koma pokhala nalo khama loposa, anatulukira kunka kwa inu mwini wake. |
| 18 |
| Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake m'Uthenga Wabwino kuli m'Mipingo yonse; |
| 19 |
| ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu; |
| 20 |
| ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira; |
| 21 |
| pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu. |
| 22 |
| Ndipo tinatumiza mbale wathu awaperekeze iwo, amene tamtsimikizira kawirikawiri ali wakhama m'zinthu zambiri, koma tsopano wa khama loposatu ndi kulimbika kwakukulu kumene ali nako kwa inu. |
| 23 |
| Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu. |
| 24 |
| Chifukwa chake muwatsimikizire iwo chitsimikizo cha chikondi chanu, ndi cha kudzitamandira kwathu pa inu pamaso pa Mipingo. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/2corinthians/008.mp3
13
8