Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo inu, anakupatsani moyo, pokhala munali akufa ndi zolakwa, ndi zocimwa zanu, |
| 2 |
| zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakucita tsopano mwa ana a kusamvera; |
| 3 |
| amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kucita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo cibadwire, monganso otsalawo; |
| 4 |
| koma Mulungu, wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco, |
| 5 |
| tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Kristu (muli opulumutsidwa ndi cisomo), |
| 6 |
| ndipo anatiukitsa pamodzi, natikhazikitsa pamodzi m'zakumwamba mwa Kristu Yesu; |
| 7 |
| kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Kristu Yesu. |
| 8 |
| Pakuti muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu; |
| 9 |
| cosacokera kunchito, kuti asadzitamandire munthu ali yense. |
| 10 |
| Pakuti ife ndife cipango cace, olengedwa mwa Kristu Yesu, kucita nchito zabwino, zimene Mulungu anazipangiratu, kuti tikayende m'menemo. |
| 11 |
| Momwemo kumbukirani, kuti kale inu amitundu m'thupi, ochedwa kusadulidwa ndi iwo ochedwa mdulidwe m'thupi, umene udacitika ndi manja; |
| 12 |
| kuti nthawi ija munali opanda Kristu, alendo a padera ndi mbumba ya Israyeli, ndi alendo alibe kanthu ndi mapangano a malonjezano, opanda ciyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi. |
| 13 |
| Koma tsopano mwa Yesu Kristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Kristu. |
| 14 |
| Pakuti iye ndiye mtendere wathu, amene anacita kutionse awiri akhale mmodzi, nagumula khoma lakudulitsa pakati, |
| 15 |
| atacotsa udani m'thupi lace, ndiwo mau a cilamulo ca kuchulako malangizo; kuti alenge awiriwa mwa iye yekha, akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kucitapo mtendere; |
| 16 |
| ndi kuti akayanianitse awiriwa ndi Mulungu, m'thupi limodzi mwa mtandawo, atapha nao udaniwo; |
| 17 |
| ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi; |
| 18 |
| kuti mwa iye ife tonse awiri tiri nao malowedwe athu kwa Atate, mwa Mzimu mmodzi. |
| 19 |
| Pamenepo ndipo simulinso alendo ndi ogonera, komatu muli a mudzi womwewo wa oyera mtima ndi a banja la Mulungu; |
| 20 |
| omangika pa maziko a atumwi ndi aneneri, pali Kristu Yesu mwini, mwala wa pangondya; |
| 21 |
| 1 mwa iye cimango conse, columikizika pamodzi bwino, cikula, cikhale 2 kacisi wopatulika mwa Ambuye; |
| 22 |
| 3 cimene inunso mumangidwamo pamodzi, mukhale cokhalamo Mulungu mwa Mzimu. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/ephesians/002.mp3
6
2