Buku Lopatulika 1922
|
| 1 |
| Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; |
| 2 |
| ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino. |
| 3 |
| Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; |
| 4 |
| kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. |
| 5 |
| Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m'ufumu wa Khristu ndi Mulungu. |
| 6 |
| Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera. |
| 7 |
| Chifukwa chake musakhale olandirana nao; |
| 8 |
| pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, |
| 9 |
| pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m'ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi choonadi, |
| 10 |
| kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; |
| 11 |
| ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; |
| 12 |
| pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. |
| 13 |
| Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. |
| 14 |
| Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. |
| 15 |
| Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; |
| 16 |
| akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. |
| 17 |
| Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. |
| 18 |
| Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, |
| 19 |
| ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; |
| 20 |
| ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu; |
| 21 |
| ndi kumverana wina ndi mnzake m'kuopa Khristu. |
| 22 |
| Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. |
| 23 |
| Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Khristu ndiye mutu wa Mpingo, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo. |
| 24 |
| Komatu monga Mpingo amvera Khristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse. |
| 25 |
| Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake; |
| 26 |
| kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau; |
| 27 |
| kuti Iye akadziikire yekha Mpingo wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema. |
| 28 |
| Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha; |
| 29 |
| pakuti munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Khristu Mpingo; |
| 30 |
| pakuti tili ziwalo za thupi lake. |
| 31 |
| Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. |
| 32 |
| Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. |
| 33 |
| Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2014/ephesians/005.mp3
6
5