Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. |
| 2 |
| Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu. |
| 3 |
| Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. |
| 4 |
| Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. |
| 5 |
| Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. |
| 6 |
| Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. |
| 7 |
| Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere. |
| 8 |
| Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika |
| 9 |
| (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). |
| 10 |
| Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. |
| 11 |
| Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. |
| 12 |
| Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. |
| 13 |
| Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. |
| 14 |
| Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.” |
| 15 |
| Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. |
| 16 |
| Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. |
| 17 |
| Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. |
| 18 |
| Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. |
| 19 |
| Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. |
| 20 |
| Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu. |
| 21 |
| Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu. |
| 22 |
| Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. |
| 23 |
| Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. |
| 24 |
| Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse. |
| 25 |
| Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo |
| 26 |
| kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. |
| 27 |
| Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. |
| 28 |
| Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. |
| 29 |
| Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake |
| 30 |
| pakuti ndife ziwalo za thupi lake. |
| 31 |
| “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” |
| 32 |
| Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. |
| 33 |
| Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/ephesians/005.mp3
6
5